Neba sizikuyenda: 1 pa 6 kwa Bullets, 6 pa 6 kwa Noma

Advertisement
Be Forward Wanderers

Timu ya mpira wa miyendo Nyasa Big Bullets ikupitilirabe kusachita bwino mu TNM super league pomwe yakwanitsa kutenga point imodzi yokha mchigawo chapakati mumasewelo awiri.

Bullets idalephera kugonjetsa timu ya Blue Eagles pa Bwalo la Nankhaka loweruka lapitali mu mzinda wa Lilongwe ndi chigoli chimodzi kwa chilowele.

Be Forward Wanderers
Be Forward Wanderers zawo zikuyenda.

Timu yafukoyi ikuoneka ngati sidapezebe njira yokhazikika yowinila italepherana ndi timu ya Master Security imene yangolowa kumene mu ligiyi posagonjetsana chigoli chilichonse pa bwalo la masewelo lalikulu mu mzinda wa Dedza.

Pa masewelo awo asanu ndi awili amene anyamata a Nswazurimo Ramadhan asewela akwanitsa kupeza ma points khumi ndi imodzi zomwe zikuwaika panambala yachitatu pa ndandanda wama team mmene akuchitila mu league yaikulu mdziko munoyi.

Bullets ikutsatanatsatana ndi timu ya Wizards yomweso ili ndi maponits khumi ndi imodzi ngakhaleso yasewela ma game asanu ndi imodzi.

Neba wa Bullets, Be forward Wanderers yamwetsa ochemelera ake wankaka mathelo omwe Bullets yawona zowawayi itakwanitsa kutenga ma points onse asanu ndi imodzi chigawo chapakati zomwe zapangitsa team imeneyi kukhala pa nambala yachiwili pa mndandanda wa ma team a mu ligi wa.

Manoma ali pa chikondwelero chifukwa yakwanitsa kupambana masewelo anayi omwe ansewela. Manoma ikufanana mapoints ndi mikango yaku Zomba, Red Lions yomwe ili pamwamba pa TNM koma yasewela masewelo asanu ndi imodzi.

Padakali pano ma team atatu okha ndi amene asewela masewelo asanu ndi awili ndipo Big Bullets ili mguluri.

Umu ndimmene mateam achitila mathelo asabata yapitayi: Loweluka Silver strikers yagonjetsa timu ya Chitipa united ndi zigoli kwa chilowele, Azam Tigers ndi Blantyre United agawana point atalephelana zigoli zitatu aliyense, Bullets idaluza kwa Blue Eagles ndi chigoli chimodzi kwa palibe, Manoma idapambadza Dwangwa United ndi chigoli chimodzi kwa palibe ndipo team ya Kamuzu Barracks idagawana point ndi team ya Civo Sporting Club atagoetsana chigoli chimodzi chimodzi.

Lamulungu timu ya Manoma idapitiliza kudzodza mateam zigoli pomwe idagonjetsa asilikali aku Zomba ndi zigoli zitatu kwa chilowele, Bullets idalepherana ndi Masters Security posagoletsana chigoli chilichonse.

Masewelo a Silver Strikers ndi Moyale Barracks adaliso opanda zigoli.

Advertisement

129 Comments

 1. sry 4 taking off topic
  what is the meaning of Milanzi?
  or what is Milanzi?
  thank you in advance 4 yo responses

 2. Mukunama guyz maule nditha kulalika apa kut kumalawi konse team yomwe ili ndi chikoka komanso masapota ambiri ndi NBB. Ndie kuluza ndi Blue eagles musati fwefwe zokuza mmawa sitinazione

 3. Ine ndinaziwa kuti anawapatsa mateam angono * 2aja kuopetsa kumenyedwa kwa akulu akulu komanso coach. Ndiye musadabwe akamachinyidwa chifukwa kwasala ziphona zokha aziona Neba.

 4. NEBA ANGODYA UDZU UDZUWAKENSO OUMA KKKKKKKKKLKK KUMPOTO WANI NANGA PAKATI WANI POINT KKKKKKKKKKKKK TEAM YA WANTHU YATHA NGATI MAKATANI PANO ATI YAKAMPANI KUTHA KKKKKKKKKKKKKLKKKKKKKKKKKKKJKK

 5. NEBA ANGODYA UDZU UDZUWAKENSO OUMA KKKKKKKKKLKK KUMPOTO WANI NANGA PAKATI WANI POINT KKKKKKKKKKKKK TEAM YA WANTHU YATHA NGATI MAKATANI PANO ATI YAKAMPANI KUTHA KKKKKKKKKKKKKLKKKKKKKKKKKKKJKK

 6. likakhala kale kwa amene tinkautsata mpirafe mkumakaona chatoma kustadium konko_tinkati bullets nkumadzulo.Charles Kafatia ndinzake uja akadziwa kt apa zada ankangopeleka penate^3kick^red card^mpaka zitheke pakavuta ikhale draw.moti kunena kwa zoona ma ligi onse 11 enieni ndi 8 atatuwa..uyu wakherere anatengako gawo powinitsa magame ena.carlsberg kt akhumudwe sponsor analinso yemweyu wakherere …lina mwa gwelo la ziwawa karelo linali limenelo

 7. pamudzi munthu ukakhala otumbwa ndi onyang’wa akakufwafwantha nkhani imakambidwa mudzionse ndiana omwe.sono iwe next door wa BFW usatutumuke lero~moyowako unkalinda kutereku~ kuganyu kumenyedwa iwe amene ukat ulowe m’bwalo akuthyola sagwada.pakakhala pachuma ndiwewadovu..

 8. wanzeru ndamuona wa bullets ndi James N’goma enanu makape”something must done”zoona, otherwise chakachino simutengako chikho ngakhale muzingoperekeza anxanu mimba.kapn tizit chingambwe chowawa zedi?nanga ndichani guyzz,he?

 9. kwa munthu ozindikila sungazilimbitse nthawi yotola ndiyomweyi.this perfomance kunena zoona ndizokhumudwitsa,mutawina pa BT UTD munkati mwanyamuka ndipo team iliyose imva zowawa ikakumana ndi BB pano mwayamba kt ikuluza si bullets yokha.ndaona ine apa nebba mutu sukugwira .MW 24 More fire ngati zamuwawa amwe tamek

 10. Kaya iwe league unayilawapo liti zaka 15 osatenga league kumayimabe pachulu ati zikuyenda admin manyazi bwaaaaaa kulimbana ndi bulets ungotaya nthawi yako bulets ilipo ndipo idakalipo utha ndiwe motoooo kuti buuuuuuuu mauleeeeee

 11. Mukat Neba Ndie Kt Can.Mukuona Za Azanu Mot Muzvere Chison Muja Anakundtsan Zakuda Asilva.Game Nd Win And Loss Palbe Akudzwka Kupambana League Imeney.Bb 4 Eva

 12. stil waiting 5 chapters of jah man ….nanga zisamangokomera kulankhula pa radio …osamangotiso dikiran kutola khobwe nd mmawa

 13. It’s a matter of understanding what football is… Lero muwina mawa ai.. Bullets had been dominating & it’s time for others to shine.. That’s football

  1. ndi mmene ziliridi komabe kamenyedwe kake ka mpira ndikotsangalatsa,what domination have you done kkkkkk? mind you this is football mkamamenya mpira ndi cholinga cha player aliyense kuti akafike pena. ngati azimenya zoti amapanga dominate ndiye kuti perfomance ya kamenyedwe ka mpira katsika wa mbuli iwe #PANGANJERENGO i think za mpira sumadzitsata

  2. U r the one who doesn’t understand what football is.. You have over aged players.. U need to rebuild wth youngsters… Fuck u & ur stupid Bullets

  1. Kodi inu a lev kani zamasewera zomwezi akazi ndevu amuna ndev kkkk zikachika hahaha zisachitike hahaha bola inu mumatulusa mbolo ku stadium game ya live on TV kukozela golo hahaha

 14. Anthu Enanunso Ndima Savage, Team Ili Pa No.3 Out Of 16 Teams, Ndiye Kusachita Bwino Kwake Kulipati Pamenepa? Ku Malawi Mburi Zinachuluka. Go Ku South Africa Mukapeza Orlando Pirates, Mamelody Sundowns, Kaizer Chiefs Amaluzanso Koma Masapota aMateam Ena Samanena Nsete Zili Kunozi, Go Ku England Mukapeza Mateam Akuluakulu Like Man-U, Nayonso Imachita Struggle But Anthu Amadziwa Kuti Ndiye Mpira Umenewo, Ndiye Zakwathu Kunozi Zotani Zokuti Usegule Page Iyi Umve Nkhani Ndi NBB, Enanunso Ndiakafansiyanji. Osamangobwira Nandolo Watchipayu Bwanji,

 15. Basis mukakhala maso pa NBB timakupasani pressure timadziwa. of all the games played amene sizinayendere ndi maule? Qua. Inu katambani nkuyang’ana kunja kungakuchereni ngati mmene kunachelerani pa BNS ndi Silver

 16. Ngakhale chaka chatha sinali bwino. Mwayi ma penalties omwe imagula aja. Tsono chaka chino ngongole zachuluka. Ndalama zoti agule ma penalty alibe. Ife sitikudabwa ndi team imeneyi. Kumbukirani kusuta kumaononga moyo.

 17. Ngati wina wabitsa magolo wagwa nayo pano ndi campany ,subwererabe uyiwale !za khobwe pa gate. Ngati siubweza magolowo akuwolera bb for life

 18. I question the capabilities of the coaches . NBB fans me inclusive are now worried now. We have had alot of encouragement from the coaches but things are now going out of hand. Something must be done& done quickly.

 19. Abisala a BB. Akungowerenga ma comments, scroll down then close the link. Si discipline ayi Koma kusowa chokomenta. Blue Eagles yathetsa kamwano konse. Ha ha hah!

Comments are closed.