Chozizwitsa chachitika, Miracle Chinga agwidwa ataba chakumwa mu sitolo

Advertisement

Mau onena kuti ng’oma yoliritsa siichedwa kung’ambika aphelezera m’modzi mwa anthu otchuka yemwe anatchulidwa kwambiri ndi anthu pakatipa atapanga zomwe aliyese samayembekezera ndipo munthu ouzidwa aliyese akumapukusa mutu opanda nyanga kuona ngati nkhaniyi ndiyabodza.

Munkhani yomvetsa chisoni komaso yochititsa manyaziyi mwana wa malemu Grace Chinga, Miracle Chinga, lachiwiri lapitali anapezeka ataba mu sitolo ina mu mzinda wa Blantyre.

Chinga: Anapezeka ataba.

Nkhani yonse ikuti mtsikanayu yemwe akuphukila kumene m’dziko la maimbidwe analowa mu sitolo ya People’s ya pa Nandos pakatikati pa mzinda wa Blantyre kuti akashope zina ndizina.

Zaululika kuti ali nkati mosankha zinthu zomwe amafunazo, mwanayu yemwe wadziwika kwambiri kamba koimba nyimbo zomwe mai ake anasiya asanazikhazikitse, anayamba kuika zinthu zina mkati mwazovala zomwe anavala.

Miracle anaiwala mawu onena kuti ukatambatamba uziyang’ana kum’mawa kungakuchere ndipo sanalingalire kuti anthu angamutulukire zomwe anapangazo.

M’modzi mwaogwira ntchito mu sitoloyi anadabwa kwambiri ndimomwe mtsikana oyimba nyimbo zopulumutsa anthuyu amayendera.

Zitatero ogwira ntchitoyu anakatsina khutu azachitetezo mu sitoloyi ndipo azachitetezowa analamulidwa kuti amuseche msungwanayu kuti atsimikize ngati anabadi podziwa kuti kutsutsa galu nkukumba.

Aliyese amene anaona izi zikuchitika anangoti kukamwa yasa atapeza botolo la chakumwa nkati mwa dilesi lomwe anavala.

Zitatero mtsikanayu yemwe akumaimba ngati mai ake omwe anatisiya chaka chatha anapempha azachitetezowo kuti angomusiya akaike zinthu zomwe anabazo pa alumale pomwe anatenga ndipo anamulora kutero.

Mtsikanayu akutuluka musitoloyi anangoti nyontcholi ngati khoswe ogwera mumvuwo pomwe anthu omwe anamva zankhaniyi anayamba kumukuwiza ndikumamuimba kuti wakuba koma mwachisomo cha Yehova sanamenyedwe ngkhale anthu ena amafuna amuonetse mazangazime.

Miracle Chinga anasankhidwa kukhala katswiri oyimba nyimbo zauzimu kuposa aliyese m’Malawi muno zinthu zomwe zinadabwitsa anthu ambiri kamba koti mtsikanayu sanatulutse chimbale chake chanyimbo ndipo pano akumangoimba nyimbo za malemu mai ake.

Advertisement

20 Comments

  1. Amalawi siyani kuweruza azanu paziko pano palibe oyela,ngati anaba ndekuti iyeyo ndi munthu chifukwa ali ndizofowoka,kodi wabwino ndi ndani,,,

    AMENE AKUZIWA KUTI MWAYINU CHIYAMBIRE SANALAKWE ATORE MWALA AGENDE

  2. This z total lie. Anthu nsanje bwanji? Musiyeni mwana ngati akukunyasani kamba kotchuka nkumaposa inu akale, ndi mmene chauta anakozera za moyo wake. Chomwe mulungu wachidalitsa mudziwe kuti simungathe kuchiipitsa mpang’ono pomwe. ZLeave her alone.

  3. She must be ashamed if she did coz she must be exemplary to the public

  4. Ngati zili zoona, tingomupempha kuti asiye chifukwa ndi nyimbo zauzimu zimene amayimbazo palibe chimene cimveke ka anthu.

  5. Musiyeni mwanayo…amene sanachimwepo yapa ndiyemwe angamunyoze mwanayu…winawe ukulembanso timbwelera tako uli mu pub…kkkkkkk oweluza ndi mulungu. Mwina walapa, mulungu wamukhululukila, iwe sudakhululuke?…lol.. a Miracle,nso nanu public figure amafunika zina ndi zina kumadziletsako….kkkkk ndakomoka…

  6. Dziko lakita kumapeto ndalama izatenga maro aliyese akufuna ndalama, koma ngati ndiboza ndiye kuti inu muri ndi soka,

  7. Photo yake ilikuti ya umbava apa mwayikapo yoti akuyima not yakuba?

  8. Siboh kumunamizila boza muthu if it true whay simukunena De name of drink musiye zachambazi

  9. Miracle wavutika, a Malawi tisamuponye miyala pali mikwingwilama ndi ma 90 Inces omwe a kukumana nawo kuchokela ku banja ndi kwa anthu oyenera kumuthandiza ku mbali yaza chuma , koma sitingadziwe
    kudziwika kapena ku tchuka zilibe ntchito. Tiyen tithandizane ku samalani anthu ngat amenewa coz alipo ena ochuluka omwe akusowa chithandizo koma kuti ndiosadziwika ngat mmene mukumudziwila Miracle Tchinga.

  10. Amalawi akufuna azimva nkhani zenizeni zopindulitsa nanga khani yongopeka tipindulanji musiyeni mwana musamunamizire,nkhani zopanda date komanso ngati mwatopa ingosiyani sitikakamiza kuti mutibweretsere nkhani…(zamkhutu mwapusi basi!)

  11. koma umboni ulipati kunama ziyani mwakula sibwino ngati mulibe ngani kupheka nkhani zabosa basi………………..

  12. This is a bad picture to the fellow Christian and put ashem on as .

  13. Sibwino kumuyipisira mbiri zanu! Mau amati muyezo omwe uyezera zako mawa azayeza iwe!

  14. Nkhani zopanda mutu zamabodza basi nkono chakumwacho chilibe dzina. UDZAFA IMFA YOWAWA

    1. Nkhani iliyapa ndi makobili osati utumiki.Malemu amai ake naonso chimodzimodzi.Kupusa kwa ife aMalawi timathamangira komwe kwalira m’futi

Comments are closed.