Chozizwitsa chachitika, Miracle Chinga agwidwa ataba chakumwa mu sitolo

20

Mau onena kuti ng’oma yoliritsa siichedwa kung’ambika aphelezera m’modzi mwa anthu otchuka yemwe anatchulidwa kwambiri ndi anthu pakatipa atapanga zomwe aliyese samayembekezera ndipo munthu ouzidwa aliyese akumapukusa mutu opanda nyanga kuona ngati nkhaniyi ndiyabodza.

Munkhani yomvetsa chisoni komaso yochititsa manyaziyi mwana wa malemu Grace Chinga, Miracle Chinga, lachiwiri lapitali anapezeka ataba mu sitolo ina mu mzinda wa Blantyre.

Chinga: Anapezeka ataba.

Nkhani yonse ikuti mtsikanayu yemwe akuphukila kumene m’dziko la maimbidwe analowa mu sitolo ya People’s ya pa Nandos pakatikati pa mzinda wa Blantyre kuti akashope zina ndizina.

Zaululika kuti ali nkati mosankha zinthu zomwe amafunazo, mwanayu yemwe wadziwika kwambiri kamba koimba nyimbo zomwe mai ake anasiya asanazikhazikitse, anayamba kuika zinthu zina mkati mwazovala zomwe anavala.

Miracle anaiwala mawu onena kuti ukatambatamba uziyang’ana kum’mawa kungakuchere ndipo sanalingalire kuti anthu angamutulukire zomwe anapangazo.

M’modzi mwaogwira ntchito mu sitoloyi anadabwa kwambiri ndimomwe mtsikana oyimba nyimbo zopulumutsa anthuyu amayendera.

Zitatero ogwira ntchitoyu anakatsina khutu azachitetezo mu sitoloyi ndipo azachitetezowa analamulidwa kuti amuseche msungwanayu kuti atsimikize ngati anabadi podziwa kuti kutsutsa galu nkukumba.

Aliyese amene anaona izi zikuchitika anangoti kukamwa yasa atapeza botolo la chakumwa nkati mwa dilesi lomwe anavala.

Zitatero mtsikanayu yemwe akumaimba ngati mai ake omwe anatisiya chaka chatha anapempha azachitetezowo kuti angomusiya akaike zinthu zomwe anabazo pa alumale pomwe anatenga ndipo anamulora kutero.

Mtsikanayu akutuluka musitoloyi anangoti nyontcholi ngati khoswe ogwera mumvuwo pomwe anthu omwe anamva zankhaniyi anayamba kumukuwiza ndikumamuimba kuti wakuba koma mwachisomo cha Yehova sanamenyedwe ngkhale anthu ena amafuna amuonetse mazangazime.

Miracle Chinga anasankhidwa kukhala katswiri oyimba nyimbo zauzimu kuposa aliyese m’Malawi muno zinthu zomwe zinadabwitsa anthu ambiri kamba koti mtsikanayu sanatulutse chimbale chake chanyimbo ndipo pano akumangoimba nyimbo za malemu mai ake.

Share.
  • Opinion