Wapolisi ataya mfuti ataledzera

Advertisement
Riffle

Apolisi mu mzinda wa Blantyre amanga ndikutsekera muchitolokosi wa polisi nzawo yemwe anataya mfuti yake ataledzera kwambiri.

Wapolisiyu anataya mfuti yake lamulungu pa 28 May, Ku Thyolo komwe mtsogoleri wadziko lino a Peter Mutharika amakakhazikitsa mfumu Ngolongoliwa kukhala mfumu yaikulu ya anthu a mtundu wa chilomwe.

Mkuluyu yemwe ndi constable Kampazanji anasankhidwa kupita nawo kumwambowu kuti akathandize kupereka chitetezo potengera kuti kumwambowu kunaliso mtsogoleri wa dziko lino.

Koma chomvetsa chisoni ndichoti m’malo mopereka chitetezo, a Kampazanji anatailira mpaka kuyamba kumwa mowa mwauchidakwa.

Malawi24 yauzidwa kuti wa polisiyu yemwe amakanika kuyenda bwinobwino kamba ka mowawo anataya mfuti yake, chida chomwe chinaenereka kumuthandiza kupereka chitetezo munthawi ya zipolowe.

Izi zinadandaulitsa apolisi amzake omwe anakatsina khutu za nkhaniyi akuluakulu omwe analamula kuti wa polisiyu amangidwe.

Padakali pano mkuluyu ali muchitolokosi cha apolisi Ku Limbe pomwe akudikila kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa.

Mfuti yomwe mkuluyu anataya yapezeka mu imodzi mwa galimoto za apolisi zomwe zinapita ku mwambowu.

Advertisement