Siife aulesi, vuto ndinu: anthu akwiyila boma powanena kuti ndi aulesi

Advertisement
Dausi

Anthu m’dziko muno atsutsa mwa ntu wagalu zomwe linalankhula boma kuti a Malawi ndi aulesi kwambiri.

Kuyankhaku kukutsatira pankhani yomwe inalembedwa ndi Malawi24 potengera zomwe linayankhula boma kudzera mwa m’neneri wake a Nicholas Dausi kuti a Malawi ndi aulesi kwambiri.

Poikira ndemanga pankhaniyi, a Malawi ambiri ati zomwe lalankhula boma kudzera mwa a Dausi ndi bodza la nkunkhuniza.

“A Malawi adayamba akupemphako kuti muwamangire nyumba? kumagona mikhukhu kudikila boma liwamangire nyumba? Chakudya a Malawi amadzilimira mvula ikabwera bwino amakhala ndi chakudya anthu, Musatiyipitsile mbiri ku maiko akunja.

“Ngati zakukanikani ingotulani pansi maudido Kamuzu ankatilemekezatu komaso amakhala akuzungulira dziko lonse la Malawi kuyambira nthawi yososa m’minda mpaka kukolola kuwalimbikitsa anthu, komaso amadziwiratu kuti chaka chino m’dziko la Malawi mukhala chakudya chochuluka chonchi,samangokhala ku nyumba kwake kumangokanda nsabwe, kenako nkumanyoza anthu kuti nda alesi,” anatero a Judith Mgoola poikila ndemanga.

Pothilira mang’ombe pa nkhaniyi a Chrissie Okwiya Phiri anati: “Wa ulesi ndaniyo? Iyeyo ndi wachibwana eti? Anthu tikugwira ntchito usiku ndi usana ndalama kuti awakakamize ma estate kuti akweze ndalama akulephera! Abwere kuno ku Thyolo ku kampani ya Makandi azaone anthu m’mene akugwilira ntchito! Ndalama zochepa chimsokho chokhacho ndiye iiiiih! Dausi usandilakwise wamva.”

Pomwe a Michael Mwanafyale Mwakalenga anati: “Amazatilimila chimanga ndiyeyo? Amatilimila mpunga, fodya, ndimbewu zinazi ndi Dausi yuuuu kapena. Kodi amalawi amadikila Dausi kuti azakolole mbewu zawo minda mwawo? Kodi sanaone a Malawi akuthamangathama ma business awo m’ma bomamu osewo tiziti amadikila a Dausi?  Kodi sanamvepo kuti anthu akufuna malipiro awo awaonjezere, kodi munthu umafuna malipiro usanagwile ntchito? Ngati munthu wamkulu akulankhula za bebe ngati izi, ife anafe tiziyankhula chani, abwana lemekezani a Malawi, sianthu opusa,” anatero a Mwakalenga.

Koma mogwirizana ndi boma a Twelike Munthali anati: “Ndife alesi. Anthu ogwira ntchito m’boma ndi anthu a kumudzi amadzuka ndi kumangowotha dzuwa.”

Anthu ambili omwe anaikilapo ndemanga pankhaniyi pa tsamba lathu la pa Facebook anati zomwe lalankhula bomazi ndizoduka mutu ndipo zilibe umboni weniweni pomwe ochepetsetsa anagwirizana ndi boma.

Advertisement

2 Comments

  1. Ngati anthu simukuwapezera misika ya mbewu kumangolimbikira fodya yemwe dziko la pansi likudana naye anthu alimbikira bwanji??? Ngati nduna ya zachuma yanena kuti ogwira ntchito mboma asayembekezere malopiro ochuluka chifukwa kugwira ntchito mboma nkongodzipereka ofuna ndalama zambiri apite ku makampani ndiye anthu alimbikira bwanji ntchito? Za ziiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiii!!!!!!!!!!!!!!!. Boma lakukanikani tulani pansi anzanu ayendetse mokomera a Malawi.

  2. Dausi ndi munthu wachipongwe, anthu akulima mbewu koma osawapezera misika inu a boma la DPP. Fodya last year mabelo agonera mmanyumbamu, ndiye ukuti anthu ndi aulesi? Foolish

Comments are closed.