20 October 2016 Last updated at: 9:17 AM

Hule amugamula kuti akagwire ukaidi zaka ziwiri atatentha nyumba ya kasitomala wake

Khoti laling’ono la Chisenjere mu mzinda wa Blantyre lagamula mayi wina oyendayenda kuti akagwile ukaidi wa zaka ziwiri atapezeka olakwa pa mlandu otentha nyumba ya bambo wina.

Khotili linamva kuti mayiyu, wa zaka makumi awiri ndi mphambu imodzi (21) anatentha nyumba ya bambo wina, bamboyu atalephera kumulipira iye atamusangalatsa.

sex-workersKhotili linamva kuti pa 27 Sepitambala chaka chino, mmayiyu amene dzina lake ndi Ellen James amamwa mowa limodzi ndi bambo wina pa malo ena otchedwa Soul City mu dera la Chileka.

Akuti awiriwa atamwa mowa anazindikira kuti akukondana ndipo anaganiza zopititsa chikondi chawo patali. Iwo anakachita za chisembwere ndipo atamaliza bamboyo anakanika kulipila. Iye anapempha kuti azalipile mtsogolo.

Akuti mayi oyendayendayo anamuvomela koma bamboyo anayamba u kavuwevuwe ndi kumangozemba ndi ndalama ya mayiyo.

A James pokupsa mtima ati anakatentha nyumba ya bamboyo ndi kuononga katundu okwanila K400,000.00.

Poweluza mulandu umenewu, oweluza anawalamula mayi James kuti akakhale kundende kwa zaka ziwiri ati chifukwa chotentha nyumba.

A James amachokela ku Balaka, mmudzi mwa a Matola. Bambo amene wawapititsa ku ndende uyu, a Polisi akana kumuulula ku gulu.  101 Comments On "Hule amugamula kuti akagwire ukaidi zaka ziwiri atatentha nyumba ya kasitomala wake"