20 October 2016 Last updated at: 9:25 AM

Tulani pansi – alangizi a Mutharika auzidwa kamba kobisa matenda a Tate wa dziko lino

Alangizi a mtsogoleri wa dziko lino alamulidwa kuti atule pansi udindo wawo ati chifukwa akhala akubisa matenda a mtsogoleri wa dziko linoyu.

Izi zanenedwa ndi mtsogoleri wa chipani cha Umodzi a John Chisi.

A Chisi ati alangizi a mtsogoleriyu akumulangiza kuti azipanga zinthu zolakwika zomwe zina mwa izo ndi kubisa matenda amene akuoneka kuti avuta mtsogoleriyu.

John Chisi

Chisi; Mutharika sakulangizidwa bwino.

“Ngakhale ali mtsogoleri wa DPP, iyeyu ndi mtsogoleri wa dziko linonso,” anatero a Chisi. “A Malawi ayenela kudziwa za umoyo wa mtsogoleri wawo, osati kunamizidwa iyayi.”

A Chisi analankhulaponso pa ndemanga zimene wathila mtsogoleri wa zipani zotsutsa mu nyumba ya malamulo amene alinso mtsogoleri wa Kongelesi a Lazarus Chakwera amene pamodzi ndi a Uladi Mussa, mtsogoleri wa chipani cha Peoples’, amati a Mutharika atule pansi udindo.

“Tiyeni titsogoze mapemphero kwa mtsogoleri wathu, tisakhale ndi dyera pa udindo,” anatero a Chisi.

A Mutharika anafika mu dziko muno lamulungu akuoneka odwala. Iwo amakanika kugwiritsa ntchito dzanja lawo la kumanja zimene zinatsimikizila anthu ambiri kuti mkuluyi ali mdziko la Amereka anadzela kuchipatala.261 Comments On "Tulani pansi – alangizi a Mutharika auzidwa kamba kobisa matenda a Tate wa dziko lino"