Tulutsani makapu tsopano, a Salima ati kukubwera Suga ngambwingambwi

Advertisement

Ija ya okumwa thiyi adzamwanso, bola osaphwanya makapu akuti ikwaniritsidwa tsopano. Kampani ya Salima Sugar yalengeza kuti tsopano ili ndi suga okwanira kufikira m’madera ambiri m’dziko muno.

Sitolo za Ekhaya, Shoprite, Chipiku, Sana, ndi zina zikuluzikulu zakhala zisakupezeka ndi sugar okwanira m’dziko  lino koma tsopano iz zikuyembekezeka kusitha.

Kudzera mwa kampani yowatumikira kuperekera katundu wawo, a Salima Sugar ati lero lino akwanitsa kale kufikitsa 30 tani  ku Tutlas mu mzinda wa Lilongwe komanso akuyembekezeka kukasiya sugar okwana  ma tani 85 ku ma shop a  Shoprite, ndiponso 30 tani ku ma shop onse a  Ekhaya.

Suga ngambwingambwi

Iwo ati izi zipangitsa kuti vuto la sugar lomwe lamanga nthenje m’dziko muno likhale mbiri yakale, ndipo alonjeza kuti iwo ayesesa kuti sugar afikile onse ngakhalenso m’malo ang’onoang’ono ogulitsira katundu.

Nduna ya Zofalitsa Nkhani, a Moses Kunkuyu, ati sugar samayenera kusowa komanso kukwera mtengo ngati m’mene anafikira panopa chifukwa chakuti ndiwofunika kwambiri pa moyo wa munthu.

Ndunayi yati kampani ya Salima Sugar imatengedwa mwachibwana popeza kuti omwe anali ngati ma shareholder a kampani yi amangogawana ndalama ndipo ndichifuwa chake zinthu zinafika poterepa.

“Lero boma linatenga umwini wa kampani yi ndipo a Malawi atha kuona kuti sugar wayamba kupezeka. Boma linatenga ma gawo onse a kampani yi ndicholinga choti ipindulire a Malawi,” adatero a Kunkuyu.

Kupatula kampani ya Salima Sugar, Illovo ndi kampani ina yomwenso imapanga Sugar m’dziko muno, Kusowa kwa sugar kwapangitsa kuti eni sitolo komanso maokala apezerepo mwayi okweza mtengo wa sugar.

Advertisement

2 Comments

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.