Abambo awiri amwalira atagunda sitima

Advertisement
Sub Inspector Rabecca Ndiwate

Abambo awiri omwe ndi a Austin Meleka komanso a Kondwani Denison amwalira atagunda sitima ya pamtunda ku Salima pamene bambo wina m’modzi wavulala kutsatira kwa ngoziyi atagona mu njanji.

Malingana ndi mneneli wa apolisi ku Salima ,a Sub Inspector Rabecca Ndiwate, wati ngoziyi idachitika pakati pa usiku wapa 5 ndi 6 January, 2025 pamene iwo adagona mu njanjimu.

Ndiwate wati, malingana ndi emwe amayendetsa sitimayi yomwe imachokera ku Kanengo kupita ku Balaka nthawi ya 12 kaloko usiku, sitimayi itafika m’mudzi mwa Steven omwe uli oyandikana ndi msika wa Mtukulamwendo, a Meleka adagunda sitimayi atagona munjanji.

Ndiwate watinso sitimayi itafika m’mudzi wa Nankuza pafupi ndi malo ochitila malonda a Katelela, idagundidwanso ndi abambo awiri omwe ndi a Kondwani Denison azaka 24 komanso a Gabriel Davie azaka 26 omwe idawapezanso atagona munjanji.

Mneneliyu wati, a Meleka komanso a Davie zidadziwika kuti atisiya atafika pachipatala chachikulu cha m’bomali pamene a Gabriel Davie awadula mwendo ndipo akulandira thandizo la chipatala.

Apa mneneliyu wapempha anthu onse okhala m’bomali kuti azitsatira malangizo omwe iwo amawapatsa ponena sitima ikuyenda ndipo asamangone munjanje kapena kuchitira malonda.