Chiyanjano Mbeza akanizidwa kutuluka pa belo

Advertisement
Mbeza

Bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe lakana pempho la belo la mkozi wa nyimbo Chiyanjano Mbeza yemwe anamangidwa poganizilidwa kuti wakhala akutulutsa ndi kufalitsa mauthenga onyoza mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera.

Malingana ndi oweruza milandu Bernadetta Kalua yemwe amawerenga chigamulo chomwe chaperekedwa ndi oweruza milandu Roderick Michongwe, chigamulochi chapelekedwa pofuna kupeleka mpata kwa apolisi kuti atsilize kafukufuku wawo pa nkhaniyi.

Malingana ndi chigamulochi, Mbeza yemwe wamangidwa Lolemba sabata ino pa 22 July, akuyembekezeka kugonaso ku ndende ya Maula kufikira Lachiwiri lino pa 30 July 2024 pomwe akawonekerenso ku bwalo la milanduli.

Izi zikubwera pomwe Lachitatu sabata ino mbali ya boma pa mlanduwu idapempha bwaloli kuti oganiziridwa yu akhalebe mmanja mwawo kwa masiku asanu ndi awiri kuopa kuti akatulutsidwa atha kusokoneza kafukufuku yemwe pakadali pano adakali mkati.

Advertisement