Mai apha ana anayi pofuna kuwachotsa mizimu yoipa

Advertisement
Malawi24

Mayi wa zaka 40 m’boma la Kasungu ali m’manja mwa apolisi atapha ana anayi powamenya Lolemba pa 22 July 2024.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Joseph Kachikho azindikira mayi oganizilidwayu ngati Ireen Banda.

Mayi Banda, akuganizilidwa kuti Lolemba lapitali wapha Funny Banda wa chaka chimodzi ndii miyezi isanu, Richard Nkhata wa zaka zisanu ndi zitatu, Samson Nkhata wazaka zinayi komanso Kelvin Banda.

Kachikho wati Banda anapha anawa pomwe analamulidwa ndi mwana wawo wa zaka zinayi yemwe akuti ali ndi mphatso ya uneneri kuti akwapule anawa ndimtengo ngati njira yowachizira ku matenda omwe amadwala.

Malingna ndi Kachikho, zotsatira za kupima matupi kuchokera pa chipatala chachikulu cha Kasungu, zasonyeza kuti anawa afa kamba kovulala kwambiri komanso kutaya magazi ochuluka.

Ireen Banda yemwe ndiwochokera m’mudzi wa Chinkhombwe mdera la mfumu yaikulu Chakhaza m’boma la Dowa, akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu wakupha.

Advertisement