M’modzi mwa anthu omwe amayankhulapo pazochitika m’dziko muno Lyford Chadza wapempha alangizi a mtsogoleri wa dziko lino kuti adzimuwunikira mtsogoleriyu mwatchutchutchu ponena kuti a Chakwera achedwa kulengeza kuti m’dziko muno muli njala.
A Chadza ati zomwe anena a Lazarus Chakwera pa uthenga wawo dzulo zimayenera kunenedwa kalekale pamene thumba la chimanga lidakwera mpaka nkumagulidwa pa mtengo wa 55,000 Kwacha osati kudikira kuti zinthu zifike poyipa.
Iwo ati pamene izi zidali chonchi, anthu ena amakangalika kuwauza anthu kuti m’dziko muno muli chimanga chokwanira zomwe zidali zabodza komanso zongofuna kumuphimba m’maso mtsogoleri’yu.
Mwazina a Chadza anati zomwe adachita a Sameer Suleiman yemwe ndi wapampando wa komitiyi ya za ulimi ku nyumba ya malamulo ponena kuti m’dziko muno mulibe chimanga zidali ndi kuthekera kopereka chithunzithunzi chenicheni kwa mtsogoleri wa dziko linoyu angakhale kuti adakakamizidwa kubweza mawu amenewa.
Pakadali pano a Chakwera ati matani a chimanga okwana 600,000 omwe mtengo wake ndi K357 billion ndi omwe afunike kuti athetse njala imene yakuta dziko pa Malawi kamba ka nyengo ya El Nino.