Mtengo wa magetsi wakwera

Advertisement
Henry Kachaje

Bungwe lowona za mphamvu zamagetsi la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA), lalengeza kuti kuyambira lero mtengo wa magetsi wakwera kuyambira lero pa 1 September, 2023.

Izi zadziwika pomwe bungweli lero linachititsa msonkhano wa atolankhani munzinda wa Lilongwe komwe amafotokoza za mtengo watsopano wa magetsiwu.

Malingana ndi mkulu wa bungwe la MERA a Henry Kachaje, kwa zaka zinayi zikudzazi, mtengo wa magetsiwu ukwera ndi K50.8 pa K100 iliyonse.

Koma a Kachaje ati magetsiwa sakwera pakamodzi koma adzichita kukwezedwa pang’onopang’ono mpaka m’chaka cha 2027.

Iwo ati kuyambira lero magetsiwa akwera ndi 18 kwacha pa 100 kwacha ili yonse zomwe ati zipangitsa kuti magetsiwa achoke pa K104.46 pa kilowati (kilowatt) kufika pa K123.26 pa kilowati.

Izi zikudza kutsatira mikumano yomwe bungwe la MERA linachititsa miyezi yapitayi m’dzikomuno yofuna kumva maganizo a anthu pankhani yokweza mitengoyi.