Alfred Gangata wasemphana maganizo ndi bwana wake Muntharika pa nkhani ya Ngongole

Advertisement
Alfred Gangata

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo cha pakati a Alfred Gangata ati aMalawi akatenga ngongole ya NEEF adye ndipo asayibweze kuti ena asapindule nayo.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa DPP-yu wanena izi dzulo pa bwalo la Chilimampunga ku Mtandire mu mzinda wa Lilongwe pomwe wati ngongole ya NEEF ndi misonkho ya aMalawi kotero akuyenera osabweza chifukwa amawadula ku katundu yemwe aMalawi amagula. Izi zikusemphaniranatu ndi zomwe ananena Bwana wawo Peter Mutharika mchaka cha 2020 ku Mjamba mu mzinda wa Blantyre pokhazikitsa Malawi Enterprise Development Fund (MEDF), pomwe anamema anthu kuti adzibweza ngongole ya boma akatenga kuti ena apindule nawo.

Mukuyankhula kwawo a Gangata ati ngongole za NEEF ndi zaboma osati chipani cha Malawi Congress ndipo ati ndalamazi zimadzera ku misonkho ya aMalawi kudutsira ku Malawi Revenue Authority (MRA) kotero aMalawi sakuyenera kubweza.

“Komansotu ndalama zimenezi ndi misonkho yanu, mukagula katundu amadula misonkho. Misonkho imeneyi ndi yomwe akugawa ngongole, a boma akutenga msonkho wanu omwe ndi kumati ngongole akugawa ndi a MCP, si ngongole za MCP zimenezi ndi ngongole zaboma.”

“Nde asakunamizeni, mwachidule ngongole zimenezi akakupatsani musabwenzenso iyayi chifukwa ndi misonkho yanu imeneyo,” anatero a Gangata polankhula.

Mchaka cha 2020 mwezi wa March, pomwe a Peter Mutharika anali mtsogoleri wa dziko lino, pokhazikitsa ngongole ya MEDF ya ndalama zokwana 18 million dollars mnthawiyo adati ngongole zimayang’ana kwambiri kupindulira achinyamata ndi amayi ndipo siziyang’ana mtundu kapena chipani ndipo kutukuka ndingongole kukuyang’ana kutukula dziko pa masomphenya a 2063.

Omwe adali nduna ya zachuma pa nthawiyo a Joseph Mwanamveka adamema anthu kuti akatenga ngongole zaboma adzibweza ndi cholinga choti ipindulire achinyamata ndi amayi ochuluka omwe angafunenso ngongoleyi.

Anthu ochuluka adzudzula mfundo yomwe alankhula a Gangata ponena kuti kutsogoza mawu oti anthu asabweze ngongole ndi kutchinga mwayi wa ngongole kwa ena.

Akatswiri ena a ndale ati mfundo ya a Gangata kuwusa anthu kuti asabweze ngongole ikhonza kudzakhala chiphinjo kuti alimbikitse anthu kubweza mu nthawi yawo ngati chipani chawo cha DPP chingadzalowenso m’boma.