Musaganize kuti mungatembenuze zinthu mu miyezi iwiri – Chimwendo Banda

Advertisement
Member of Parliament

Mlembi wamkulu wachipani cha Malawi Congress (MCP) Richard Chimwendo Banda yemwenso ndi mkulu wa zokambilana mnyumba ya malamulo wati kukhala kovuta kuti andale ena athe kutembenuza zinthu mu miyezi yochepa pamene chisankho chayandikira ngati zakanika mu zaka zinayi.

A Banda amayankhula izi mnyumba ya malamulo lachinayi mu mzinda wa Lilongwe pomwe amatsilira ndemanga pa bill no.17 ya 2025 yokhudza nkhani za mu ubongo “mental health.” Iwo alangiza aphungu anzake kuti asawononge chuma chawo chonse kukopela anthu, kuwakondweletsa pomwe akanika kuwapangila zinthu mu zaka zinayi ndi theka.

Phiri
Phiri: Aphungu ena akufunika thandizo la mu ubongo.

Chimwendo Banda wati ngati aphungu anakanika kukondweletsa anthu omwe amawatumikira, ngakhale atayesetsa bwanji mu miyezi inayi palibe chomwe chingasinthe, ndipo wachenjeza aphungu kuti asagwe mu ngongole za nkhani-nkhani, za katapila zomwe zingakhudze maganizo awo (mental health).

“Musagwiritse ntchito ndalama zanu zonse kupangira campaign, chifukwa vuto lalikulu ndi lakuti ngati mwalephera kupanga zinthu mu zaka zitatu/ zinayi zapitazi, ngakhale mutayesetsa bwanji kuchita zinthu mu miyezi inayi ikubwerayi palibe chitachitike, ndudziwa kuti zozizwa zimatha kuchitira,” a Banda anatero.

A Ben Phiri phungu wa Thyolo Central wati poyamba mnyumba ya malamulo munali anthu olongolora koma pano afatsa zomwe zutanthauza kuti zinazake mu ubongo wawo sizikuyenda bwino ndipo chilipo chikuwazunza ndipo ati bill ya Mental health yabwera mu nthawi yake pomwe masankho ayandikira.

A Phiri omwe ati ndi katswiri othandizanso nkhani za mavuto a mu ubongo, ati alankhula ndi aphungu angapo ndipo akuona kuti aphungu ena ndi ofunika thandizo la mu ubongo ndithu.

Iwo anati zina mwa zomwe zikuwadya aphungu minofu ndi ngongole, nkhawa, komanso kuphyinjidwa ndi zofuna za anthu a ku madera kwawo.

Apo a Phiri anapempha unduna wa za umoyo kuti ayesetse kusaka ndalama zomwe zithandize kwambiri kuti zomwe zili mu bill ya mental health zikwanilitsidwe.

Mwa zina bill- yi ikuyang’ana zobweretsa ma ufulu kwa anthu omwe ali ndi mavuto a mu ubongo, kulolerana, ungwiro wawo komanso kuwonetsetsa kuti anthu omwe ali ndi mavuto a mu ubongo akupeza zonse zoyenera monga wina aliyense.

Bill yi ikukambanso za kukhazikitsidwa kwa Mental health board yomwe idziyang’anira zonse zokhudza nkhani za mavuto a mu ubongo komanso kuphatikiza omwe akuvutika ndi matenda a mu ubongo mdziko  muno.