
Bungwe loyendetsa masewero a mpira wamanja mdziko muno la NAM, lati ndilokondwa ndi luso latsopano lomwe lapeza mmadera osiyanasiyana.
Mlembi wamkulu wa bungweli, Yamikani Kauma wayankhula izi lero pa bwalo la zamasewero la Bingu, mumzinda wa Lilongwe komwe atsikana okwana makumi asanu ndi atatu (80), amamaliza m’bindikiro.
M’bindikirowu unayamba lamulungu lapitali, pa 20 Epulo ndipo cholinga chake chinali kusula atsikanawa, powapatsa ma phunziro a mmene akuyenera kusewelera mpira wa manja.
“Tinayenda mmaboma onse kusaka atsikana achichepere omwe ndiwotalika ma mita 1.7 kupita mmwamba, kaya anasewerapo mpira kapena ayi ndipo tinapeza pafupifupi atsikana okwana 250”
“Ku m’bindikiro wathu oyamba tinatenga atsikana 80 ndipo ndife okondwa kuti ambiriwa anasewerapo mpira chomwe chikutilimbikitsa kuti sitikhala ndivuto kwambiri powakonzaso kuti afike pa mulingo omwe tikuwufuna”.
Malingana ndi Kauma, ambiri mwa atsikana omwe asankhidwa ndi apakati pa zaka 15 ndi 20 ndipo ndiwochokera mmaboma onse amdziko muno.
Ngati njira yowayang’anira atsikanawa pomwe akubwelera mmakwawo, Kauma anati NAM yapempha unduna zamaphunziro komaso bungwe loyang’anira masewero mma sukulu, la MASSA kuti apeleke mwayi wamaphunziro kwa atsikanawa mumasukulu a ukadaulo (schools of excellence). Ndipo kwa omwe sapita ku Sukulu, NAM yapempha ma timu amdziko muno kuti atenge osewerawa.
Kwamilungu iwiri, NAM yakhala ikusaka atsikana atali-atali mmaboma onse, kudzera mu thandizo la ndalama lochokera ku Kampani ya NICO.
By Eric Chiputura