
Mphunzitsi wamkulu wa timu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira watulutsa m’ndandanda otsiliza wa osewela a timuyi okwana 30 omwe wati ndi amene akufuna kutengetsa nawo chikho cha 2025 TNM Super League chaka chino, monga limakhalira khumbo la aliyense.
Mpinganjira wayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani lero omwe anachititsa ku Lali Lubani mu mzinda wa Blantyre komwe wati adayamba kukonzekera miyezi iwiri yapitayo ndi osewela oposa 35 koma wasefa ena ndi kutsala ndi omwe walengeza lero kuti agwire ntchito mukuthamanga kwa mu 2025.
Mphunzitsiyu watinso osewela wakale Alfred Manyozo JNR yemwe adamusankha poyamba kukhala ozukuta m’mene osewela akuchitira tsopano walekana nawo udindowu chifukwa cha sukulu yomwe akupanga mu mzinda wa Lilongwe ndipo m’malo mwake ayikapo Anstey Chinombo.
Wanderers yomwe inatsiliza mpikisano wa chaka chatha pa nambala yachiwiri, chaka chino iyamba masewelo ake ndi timu ya Blue Eagles Lamulungu pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.
Osewela onse omwe atumikire Wanderers ali motere:
Goalkeeper
Richard Chipuwa
Chancy Mtete
Dalitso Khungwa
Vincent Mdoka
Defenders
Masiya Manda
Stanley Sanudi
Timothy Silwimba
Lexon Osman
Emmanuel Nyirenda
Lawrence Chaziya
Peter Cholopi
Chimwemwe Nkhoma-
Samson Banda
Ahmed Kung’unde
Midfield
Nanison Mbewe
Daniel Kudomto
Felix Zulu
Blessings Singini
Dave Chikaonda
Isaac Kaliati
Wisdom Mpinganjira
Wallas Adam
Chifuniro Kamenya
Vitumbiko Kumwenda
Francisco Madinga
Gaddie Chirwa
Strikers
Clement Nyondo
Sama Thierry Tanjong
Promise Kamwendo
Blessings Mwalilimo