Bata tsopano labwelera pomwe apolisi ku dela la Makanjira m’boma la Mangochi awombela pa mimba ndi kupheratu Peter Davis wa zaka 25 lero kutsatira mkangano omwe unabuka pakati pawo m’bandakucha wa lero pa malo ena omwera chakumwa cha ukali.
Malingana ndi a Alick Salama m’modzi wa ochita malonda omwe anawona izi zikuchitika, ati apolisi amafuna kutseketsa malo omwera mowawo ati popitiliza nthawi yopangira bizinesiyi.
A Salama ati anthu omwe anali pa malopa sadakondwe ndi chikonzelo chotseka malowa chomwe chinabwera ndi apolisiwa zomwe zinadzetsa mkangano ndi kusagwirizana.
“Mkangano utakula, a polisiwa anawomba mfuti kangapo ndipo chimodzi mwa zipolopolo chinafikira pamimba pa Devis yemwe anafera pa chipatala cha Mangochi. Anafotokoza a Salama.
Mfumu Makanjira inati kuphedwa kwa Peter Davis kwabweretsa chipwilikiti mderali, pomwe anthu amasaka apolisiwa kufuna kuthana nawo.
Ena omwe Malawi24 yalankhula nawo kuchokera ku Makanjira ati anthu awononga katundu wambirii kuphatikiza kuwotcha njinga zamoto komanso nyumba zomwe ena mwa apolisiwa amakhala, ndipo ati kufikira masana wa Lamulungu ku delali kunali apolisi ambiri a PMS.
Poyankhura ndi Malawi24 oyankhulira polisi ya Mangochi a Amina Tepani Daudi bata tsopano labwelera pamene apolisi apita kale kuthandizira kuti bata libwelere mdera la Makanjira, ndipo ati afotokoza za momwe zonse za ngoziyi zakhalalira, komanso katundu amene wawonongedwa.
Masiku awiri apitawo, anthu ena anakhapa ndi kupha mwankhanza wamkulu wa apolisi ya Chiponde Border Benjamin Munthali boma lomweli, pamene amafuna kukakhazikitsa bata pomwe panali mkangano wa anthu a m’mudzi ndi anuwake a estate ya Chipunga nkhani zokhudza malo.