
Oimba odziwika bwino m’dziko muno, Dan Lu, yemwenso pakatipa wakhala akuyimba nyimbo zotamanda mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP), Lazarus Chakwera, wakwidzingidwa ndi apolisi masana a lero ku Lilongwe.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani ku polisi ya Lingadzi, Maria Kumwenda, watsimikiza za nkhaniyi ngakhale wakana kuyankhulapo zambiri.
Malipoti amene tapeza akusonyeza kuti mkhulang’ona pa maimbidweyu akumuganizira kuti anamenya ogwira ntchito ku Water Board pamene amafuna kudula madzi ku nyumba kwake ku Area 49.