Bambo anjatidwa kamba kopha mwana

Advertisement
Chiradzulu Police

Apolisi m’boma la Chiradzulu amanga John Tebulo wazaka 43 pomuganizira kuti wapha mwana wazaka zitatu pachifukwa choti anadutsa m’munda mwake.

Malinga ndi m’neneri wapolisi ya Chiradzulu, Cosmas Kagulo, makolo a mwanayo analawilira kumunda kumusiya akugona kamba koti mundawo unali pafupi.

Atadzuka, mwanayo anayamba kulondola makolo akewo ndipo anadutsira m’munda mwa Tebulo. 

“Izi sizinamusangalatse mzibamboyu ndipo anatenga chikwanje ndikuyamba kukhapa mwanayo, yemwe anthu anathamangira naye kuchipatala koma mwatsoka, anali atamwalira,” anatero a Kagulo.

A Kagulo anapitiliza kunena kuti apolisi anapulumutsanso woganiziridwayo kamba koti anthu a m’mudzi anayamba kumumenya.

Pakadali pano, mzibamboyu akulandira thandizo kuchipatala atavulala kwambiri.

Izi zachitika m’mudzi wa Likhomo, mfumu yaikulu Sandrack m’boma la Chiradzulu.

Advertisement