Azibambo anayi akasewenza kundende kamba kokuba

Advertisement
Lilongwe

Bwalo la milandu mu mzinda wa Lilongwe lagamula kuti azibambo anayi akakhale ku ndende zaka za pakati pa 13 ndi 20 kamba kotchola nyumba ina ku Area 49 komwenso adakhapako anthu, kuphatikiza ana awiri.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu wati anthuwa anali mugulu loposa anthu khumi lomwe lidakaba ku nyumbayo cha m’ma 1 koloko usiku pa 25 December chaka chatha.

Gululo ati lidanyamula zida zosiyanasiyana kuphatikazapo zikwanje ndi zitsulo. Anthuwo adathyola nyumbayo ndi kukhapamo anthu pofuna kuwakakamiza kuti apereke ndalama, mafoni ndi makompyuta.

Achigalu ati mbavazo zidaba K25 000 ndi mafoni awiri, zonse pamodzi zokwana K600 000. Apolisi adagwiritsa ntchito ukadaulo wawo pofufuza ndi kugwirapo anayiwa mu January.

A Yohane Daniel (26) ndi Evance Lufeyo (39) akakhala kundende kwa zaka 20, a Madalitso Soniyala (37) akakhalako zaka 18, pamene a Dickson Mavuto (30) akakhalako zaka 13.

Woweruza milandu Senior Resident Magistrate Bracious Kondowe adagwirizana ndi woimira boma pa mlanduwu, a Evance Kantukule, kuti anthuwa amafunika chilango chokwima kamba koti adachita zinthu zoopsa.