CDEDI yamema atsogoleri a zipani zotsutsa kukachita nawo zionetsero Lachinayi lino

Advertisement
Activist Sylvester Namiwa who leads Cdedi

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI), layitana atsogoleri azipani zotsutsa boma kukachita nawo zionetsero Lachinayi lino posakondwa ndi vuto lakusowa kwa mafuta komaso mgwirizano wa MEC ndi kampani ya Smartmatic. 

Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani munzinda wa Lilongwe, mtsogoleri wa CDEDI Sylvester Namiwa, waitana mtsogoleri wa chipani cha UTM, Dalitso Kabambe, Atupele Muluzi wa UDF, Enock Chihana wa AFORD, Kondwani Nankhumwa wa PDP komaso Peter Mutharika wa DPP, kuti akatenge nawo gawo pa zionetserozi.

“Nanu a Richard Chimwendo Banda, nanunso mubwere ku ziwonetserozi, vuto la mafutawali silikuona kuti uyu ndi wa MCP kapena ayi,” watero Namiwa. “Dr Joyce Banda, inutu munakwanitsa kuthetsa vuto la kusowa kwa mafuta kwa kanthawi kochepa, Inu landirani maluwa anu, mubwere ku zionetsero za Lachinayi lino.”

Namiwawa wat ziwonetserozi ndizofuna kukakamiza nduna yowona za migodi ndi mphamvu a Ibrahim Matola komanso mkulu wa bungwe la MERA Henry Kachaje, atule pansi udindo ponena kuti alephera kuthetsa vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto.

Kuwonjezera apo, iye wati zionetserozi zikufunaso kukakamiza bungwe la MEC kuyimitse kaye kalembera wa zisankho za chaka cha mawa posasangalatsidwa ndi kampani ya Smartmatic yomwe wati ndiyokayikitsa.

Advertisement