Nduna yoona zokopa alendo m’dziko muno a Vera Kamtukule yatsimikizira anthu okhala m’boma la Likoma kuti Chilumba cha Likoma sichikugulitsidwa.
A Kamtukule anena izi pomwe unduna wawo umakumana ndi akulu akulu a m’boma la Likoma pofuna kuwafotokozera chilungamo chenicheni pa nkhani zomwe zimamveka kuti Boma likufuna kugulitsa malowo.
Malinga ndi ndunayi, boma lilibe ganizo lililonse lofuna kugulitsa Chilumba cha Likoma, ndipo zomwe zimamvekazo ndi zabodza.
Iwo anapitiliza kunena kuti noma limapanga zinthu zake motsatira malamulo a dziko lino komanso kulemekeza ufulu wa anthu .
A Kamtukule awuza anthu pa mkumanowu kuti munthu yemwe amatchulidwa Kuti afuna kugula malowa yemwe dzina lake ndi Augustus anawonetsa chidwi kuti azichita malonda pamalopa , koma boma linakana pempho la mkuluyu chifukwa silimatsata malamulo a dziko lino komanso fundo zotukula malowa.
Iwo anatiso noma lakhala likupeleka mwayi kwa anthu ofuna kuchita malonda pa malowa maka a mayiko a kunja kuyambira chaka cha 2022.