Chakwera anandisankha chifukwa ndimatha kupempha – watelo Usi

Advertisement
Malawi Vice President Michael Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Michael Usi wati iye anasankhidwa pa udindo wake ndi mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera chifukwa choti iye ndi namatetule pankhani yopemphetsa kwa azungu. 

A Usi ayankhula izi ku mayambiliro a sabata ino ku Ndirande munzinda wa Blantyre pomwe amamalizitsa maulendo awo ochezera anthu m’misika yosiyanasiyana mchigawo cha kummwera.

Iwo ati, “M’mene bwana Chakwera amandisankha amadziwa bwino lomwe kuti chimodzi cha ukatswiri wa ine ndi kupempha ndalama ku mayiko akunja, kupempha ndalama kwa anthu ena chifukwa ndagwira ntchito ku ADRA komwe ntchito yanga inali yopempha ndalama kwa azungu.”

Popelekera chitsanzo za unamandwa wawo pa nkhani yopemphapempha, a Usi ati chiwasankhileni paudindowu apempha kale makampani angapo kuphatikizapo kampani yofulura mowa ya Chibuku kuti athandize kukozaso nsika wa Ndirande omwe ati ukusowekera zinthu zochuluka.

Pa nsonkhano omwewo, a Usi ati iwo pamodzi ndi malemu Saulos Chilima akhala ali m’boma kwa zaka zinayi choncho sizoona kuti akatembenuke lero ndikutuluka monga m’mene akuluakulu ena a chipani chawo cha UTM akufunira. Iwo ati akufuna ayesetse kukwanilitsa zimene malemu Chilima analonjeza anthu m’dziko muno.

Usi anasankhidwa ndi Chakwera kukhala wachiwiri wake pa 20 June 2024 kutsatira imfa ya Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu pa 10 June chaka chino pangozi ya ndege yomwe inagwa m’nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.

Advertisement