Namondwe Jude wafika ndi chifunga komanso mvula yowaza mu mzinda wa Blantyre

Advertisement
Rains

M’mawa wa tsiku la lero pa 10 March, 2025, dzuwa silinaoneke mu mzinda wa Blantyre, mvula yowaza ikugwa pakadali pano ndipo ndi yomwe yakuta mzindawu.

Kudzera ku nthambi ya boma yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi yati mvulayi ikhala ikugwa kuyambila pa 10 March, 2025 m’madera a chigawo cha kum’mwera. 

Nthambiyi ikuchenjeza anthu amene akukhala madera okhudzidwa ndi Namondweyu kuti akhale osamala.

Tili pa nkhani yomweyi, unduna wa za maphunziro a sukulu za pulayimale ndi sekondale wayimitsa kaye sukulu za pulayimale, sekondale ndi ma college kufikira pa 14 March ngati njira imodzi yoteteza ana a sukulu ku Namondweyu.