Kugwira ntchito kuposa boma kugwetsera apolisi 6 ku ndende pa mlandu wakupha

Advertisement
Lilongwe High Court

Oweluza milandu ku bwalo lalikulu la milandu ku Lilongwe, Chifundo Kachale, wakhazikitsa tsiku la pa 28 February kukhala tsiku lomwe akateme apolisi asanu ndi m’modzi (6) ndi chilango, bwalo litapeza kuti apolisi ogwira ntchito m’bomawa adapha a Buleya Lule.

Izi zadziwika lero pomwe bwalo linakumananso kumvapo pa za chilango zomwe zimathandizira oweluza kudzapeleka chilango choyenera kwa olakwa pa tsiku la chilango.

Bwalo la milandu mu mzinda wa Lilongwe m’mwezi wa December 2024, lidagamula apolisi asanu ndi m’modzi-wa kuti ndi omwe adapha Buleya Lule pa nthawi yomwe anali mchitolikosi cha apolisi mchaka cha 2019.

Oweluza Kachale adati a Paul Chipole, Ikram Malata, Innocent Lwanda, Richard Kalawire, Maxwell Mbuzi ndi Abel Maseya bwalo lidawapeza olakwa pa mulandu wakupha, kuvulaza munthu komanso kulekelera pa ntchito pomwe adalephera kuteteza a Lule komanso adagwilitsa ntchito nkhanza kuti a Lule avomele.

M’modzi mwa oyimila opalamula mlandu Lugano Mabutwa ati akukhulupilira kuti ma umboni ena omwe apelekedwa m’bwalo lero pa chilango athandizira kuti chilango pa owayimilira awo chikhale chomvelera.

Oyimira boma pa mlanduwu a Dzikondianthu Malunda ati ma umboni akhale akuwawunika ndi kuwazukuta ndi kupeleka maganizo awo pa m’mene oweluza apelekere chilango ndipo oweluza Chifundo Kachale walamula kuti mbali zonse zikhale zitapeleka zolemba zawo zonse pofika pa 20 February 2025.

Pomwe a Lule adamwalira, anthu ambiri adati pakufunika kuwoneka chilungamo pa imfa ya a Buleya Lule omwe adamwalira mchitolokosi cha apolisi pomwe ankasungidwa chifukwa choganizilidwa kuti adasowetsa mwana wa khungu la chi alubino m’boma la Dedza.

Pomwe mlandu unali kupitilira a Kachale adagamula kuti apolisi ena anayi omwe ndi a Evelista Chisale, Steven Mashonga, Wallen Joshua Chavinda ndi Chifundo Chiwambo alibe mlandu oti ayankhepo chifukwa padalibe ma umboni okwanila kuti adatenga nawo mbali yokupha a Lule.

Ma umboni a chipatala omwe akatswiri owunika matupi adachita adawonetsa kuti a Lule adaphedwa mwa nkhanza zomwe mwa zina ati a Lule adamenyedwanso ndi chitsulo chozungulira.