Gulu la Mbadwa zokhudzidwa lidzudzula m’chitidwe ogwilitsa ntchito bungwe la ACB molakwika

Advertisement
Concerned Citizens

Gulu la Mbadwa Zokhudzidwa ladzudzula mchitidwe ogwilitsa ntchito bungwe la ACB molakwika polipatsa uthenga opotoka ndi cholinga chofuna kuipitsilana mbiri maka pamene zipani zikupita ku misonkhano yaikulu – convention. 

Polakhula kwa atolankhan dzulo modzi wa akuluakulu a gululi a Fredrick Billy Malata anati Pali anthu ena omwe akugwilitsa ntchito ACB pofuna kuipitsilana mbiri maka pamene chipani cha MCP chikupita ku msonkhano wake waukulu komwe mwazina nthumwi zikasankhe adindo.

A Malata alankhula izi pamene pali kupikisana pa mipando yonona mchipani cha MCP monga wa mlembi wamkulu komanso wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani. 

“President, Lazarus Chakwera akuyenera atenge gawo poonetsetsa kuti kugwebana kumeneku kwatha chifukwa MCP ili ndi ntchito yaikulu yosamalira ma million aanthu omwe ali mdziko muno,” adatero a Malata. 

Iwo adatinso kugawa ndalama pa nthawi ya campaign sikolakwika kaamba koti malamulo ali ndi chindunji cholozeka pa nkhaniyi.

Agape Khombe omwe ndi m’modzi wa akulu akulu a gululi anati anthu asiye kugwiritsa ntchito imfa ya yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Chilima ngati chida chofuna kukwanilitsa zolinga zawo pa ndale.

Malingana ndi a Khombe chichitikireni ngozi ya ndege yomwe inapha a Chilima komanso anthu ena asanu ndi atatu, andale ena atengelapo danga lofuna kugwetsa boma la Dr Lazarus Chakwera zomwe ndizolakwika.

Gululi ladzudzulanso magulu ena a anthu omwe ati akumafalitsa nkhani zabodza kudzera pa masamba a mchezo, popereka chitsanzo cha Limpopo FM komanso Bakili Muluzi TV ponena kuti zikuononga mbiri ya anthu ena.

Advertisement