Chipani cha United Transformation Movement (UTM) chati chipani cha Malawi Congress (MCP) chidamugwiritsa ntchito yemwe anali mtsogoleri wawo malemu Saulos Chilima ngati madzi othetsera ludzu lawo lofuna kulowa m’boma kenaka “mkumutafuna.”
Izi zili mu kalata yomwe chipani cha UTM chatulutsa Lachisanu pa 12 June 2024 yomwe wasayinira ndi mlembi wake Patricia Kaliati pomwe chipanichi chalengeza kuti chatuluka mugwirizano wa Tonse.
Mukalatayi, UTM yati malemu Chilima adali ndi umunthu komaso adawonetsa kudzichepetsa pomwe adalora kuti a Lazarus Chakwera omwe ati analibe upangiri pankhani yolamulira dziko akhale patsogolo pawo, iwo pambuyo.
Chipanichi chati ndi za chisoni kuti kuyambira tsiku loyamba, malemu Chilima adanamizidwa, adanyozedwa, kumanidwa ntchito, kumangidwa, komanso kutukwanidwa masana ndi usiku zomwe chati nchipongwe chachikulu.
UTM yati, “Izi zidadziwika kuti MCP idafuna kuti Dr. Chilima awaolotse kenako akawatafune. Ndeno lero, polingalira zonsezi tikunenetsa kuti mu mgwiriza wa chinyengowu, mu mgwirizano wa ‘ndiolose ndikakutafune ife ngati chipani cha UTM tatulukamo.”
Chipanichi chati tsogolo lowala lomwe malemu Chilima ankalikamba kwambiri silinafe, koma chati tsogolo lowalari lidzafika ngati anthu m’dziko muno angatengapo gawo povota mwa nzeru pa chisankho chomwe chichitikeso chaka cha mawa chino.
Ngakhale chipanichi chati chili ndi mafuso ochuluka pa imfa ya yemwe adali mtsogoleri wake Chilima chati, “Sitikufuna kumema anthu kuti pachitike ziwawa koma tikufuna kuti tidziwe chilungamo chonse mwansanga. Ndife chipani chodekha monga tidaphunzilira kwa mtsogoleri wathu motero tipitilira kutero.”
Malemu Chilima pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu adafa pa 10 June chaka chino pomwe ndege yomwe adakwera akupita ku maliro a Ralph Kasambara ku Nkhata Bay, idagwe m’nkhalango ya Chikangawa.