Mabungwe a National AIDS Commission (NAC) ndi Pharmacy and Medicines Regulatory Authority (PMRA), ati ndi okhumudwa ndi kufala kwa mchitidwe ogulitsa komaso kusatsa mankhwala ponama kuti ndi ochiza matenda a Edzi.
Kudzera m’kalata yomwe mabungwewa atulutsa Lachitatu, kafukufuku akusonyeza kuti kudzera m’masamba a mchezo monga TikTok, Facebook komanso WhatsApp, anthu ambiri akumanama kuti ali ndi mankhwala ochiza matenda a Edzi.
NAC ndi PMRA ati kafukufuku wawo, “wapeza kuti pali akamberembere ena omwe akumagula mankhwala odziwika mma pharmacy, kumatula/kuchotsa zolembedwa pa mankhwalawo ndi kumata ma sitika olemba kuti Gammora, kenaka nkuyamba kutsatsa mankwalawo nkumawauza anthu kuti ndi katemera wa mankhwala omwe amapheratu HIV.”
Mabungwewa ati ili ndi bodza lankunkhuniza ponena kuti pakadali pano mankhwala ochiziratu Edzi kulibe ndipo ati mauthenga achinyengo ngati amenewa ali ndi kuthekera koika miyoyo ya anthu ochuluka omwe ali ndi HIV pa chiopsezo.
Pa chifukwa ichi mabungwe a NAC ndi PMRA achenjeza anthu onse kuti kufalitsa uthenga wabodza okhudza HIV ndi Edzi ndi mulandu malinga ndi gawo 25 la malamulo a bungwe la NAC komanso gawo 98 la malamulo a bungwe la PMRA.
Mabungwewa ati, “Apitirira kugwira ntchito ndi nthambi zina za boma monga Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) komanso a Polisi ndi cholinga chakuti milandu yonse yokhudza kugulitsa mankhwala abodza ochiza HIV kuphatikizapo a Gammora ifufuzidwe ndipo onse omwe akuchita izi agwide ndi kuzengedwa mlandu.”
Pakadali pano, anthu omwe anapezeka ndi HIV ndipo akumwa ma ARV akuchenjezedwa kuti asanamizidwe kuti kutsika kwa chiwerengero kapenanso kusapezeka kumene kwa HIV mthupi mwawo ndi kamba ka mankhwala achinyengowa.
Pa 13 March 2024, bwalo la milandu ku Mangochi lidapeza amayi awiri olakwa ndi kuwalipilitsa chindapusa cha ndalama zokwana pafupifipi K2.5 miliyoni aliyense pa mlandu ogulitsa mankhwala a jakiseni a gentamicin omwe amati ndi katemera wa Gammora yemwe amapheratu HIV.
Kupatula apo, pa 13 June 2024, bwalo la milandu ku Mwaza lidalamula bambo wina wa zaka 32 kukakhala ku ndende kwa miyezi khumi ndi isanu (15) pa mlandu ogulitsa mankhwala amapilitsi osadziwika omwenso amati ndi Gammora ochiza HIV.