Yesetsani ndalama ya fizi idzioneka phindu lake – sukulu zomwe sizaboma zalangizidwa

Advertisement
Ernest Kaonga

Sukulu zomwe sizaboma zalangizidwa kuti ziyesetse kuti ndalama za nkhani nkhani zomwe ophunzira amapeleka ngati fizi zidzioneka phindu lake pokhozetsa bwino pa mayeso a boma, ponena kuti makolo amakhala atadutsa m’zikhomo kuti apeze ndalamazo.

Izi ndimalingana ndi m’modzi mwa anthu odziwika bwino pa nkhani zopita pa tsogolo maphunziro m’dziko muno Ernest Kaonga omwe ati chimene makolo amafuna akamapeleka ndalama za fizi, ndi zotsatira zabwino kuchokera kwa ana awo.

Iwo ati pachifukwa ichi sukulu zomwe ndizoyima pazokha zikuyenera kuchilimika kuyika njira zabwino zomwe zingathandizire kuti ophunzira awo adzikhoza bwino pa mayeso a boma komaso adzitengedwa kukaphunzira m’sukulu za ukachenjede za boma.

“Makolo akuvutika kuti apeze ndalama zolipilira ana awo fizi makamaka m’sukulu zomwe sizaboma, choncho zingakhale zosangalatsa ngati opeleka fiziwo atamawona phindu la ndalama zawo zomwe amapelekazo.

“Phinduli ndikuphatikizapo kukhozetsa bwino komaso kuchilimika kuti ophunzira ambiri ochokera m’sukulu zoyima pazokha adzisankhidwa kupita ku sukulu zaukachenjede. Ife tikumema sukulu zomwe sizaboma kuti zichilimike ndithu,” atelo a Kaonga.

Iwo ati izi ndi zomwe zapangitsa sukulu yawo kukhala yokhayo yomwe yatumiza ophunzira ochuluka ku sukulu zaukachenjede, pomwe ophunzira ena 25 awasankhiraso ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (LUANAR), kuonjezera pa ophunzira 246 omwe adasankhidwira m’mayunivesite osiyanasiyana mwezi watha.

Pomaliza Kaonga walonjeza kupitiliza kuthandizira boma pa masomphenya okweza maphunziro m’dziko muno, ndipo wati mwa zina apitiliza kubweretsa mfundo zapamwamba zomwe zingapangitse ophunzira kuchilimika.

Advertisement