Wapha mamuna wake atamukoka maliseche 

Advertisement
Malawi24

Apolisi ku Chitipi m’boma la Lilongwe amanga mayi wina wa zaka 24 kamba komuganizira kuti wapha mamuna wake a Misheck Byson powakoka maliseche.

M’neneli wa apolisi m’bomali a Sub Inspector Hastings Chigalu, atsimikizira za nkhaniyi ndipo ati mayiyu ndi Ruth Nkhoma.

Malingana ndi a Chigalu, ati pa 17 June mwezi uno awiriwa adakangana pankhani yokhudza ndalama yokwana 40 sawuzande zomwe mamunayu adatenga ndikukamwera mowa.

Zitachitika izi mayiyu atazindikira kuti wapha mamuna wakeyo, iye adatenga chingwe ndikumangilira mamunayo pa zenera ndicholinga choti anthu akaona malirowo aziti mamunayo wachita kudzipha.

Lachitatu pa 19 June apolisi adapita kukamanga mayiyu kuti akamaufunse mafunso. Apa mayiyo adafotokozera apolisi kuti mamunayo adatenga ndalama yakeyo popanda chilolezo.

Iye atapanikizidwa ndi mafunso mpamene mayiyu amaulula kuti mamunayo adachita kumupha kamba ka mkwiyo.

Mayiyu amachokera m’mudzi mwa Thonyiwa kwa mfumu yaikulu Nsabwe ku Thyolo, pamene malemuwa amachokera m’mudzi mwa Nyenyezi kwa mfumu yaikulu Malema ku Nsanje.

Advertisement