Tadikira tsopano ndi mfulu

Advertisement
High Court in Mzuzu

Bwalo lalikulu lozenga milandu ku Mzuzu lathetsa mlandu omwe limamuzenga Tadikira Mafubza Mutharika komanso anthu ena asanu ndi awiri.

Tadikira yemwe ndi mwana wa a Gertrude Mutharika anamangidwa pamodzi ndi anthu asanu ndi awiriwa powaganizira kuti anatengapo gawo pa milandu yozembetsa komanso kupha anthu makumi atatu omwe amaganizilidwa kuti ndi nzika za dziko la Ethiopia ndipo zimafuna kulowa m’dziko muno mozemba komanso mopanda chilolezo.

Koma mu chigamulo chake, oweluza milandu a Gladys Gondwe anati bwalo lakanika kupeza umboni ogwirika pa kukhuzidwa kwa Tadikira komanso anthu enawa pa imfa ya anthuwa.

Matupi a anthuwa adapezeka atakwililidwa mu nkhalango ya mtangatanga m’boma la Mzimba.

Advertisement