Mayi Triephonia Mpinganjira, omwe amadziwika bwino ndi kuthandiza ochepekedwa m’dziko muno, agulira namwino opuma nyumba ya ndalama zokwana 30 miliyoni Kwacha.
Mayi Ireen Tembo, a zaka 66, anali namwino ndipo agwira ntchito zipatala zochuluka kuphatikizapo Queen Elizabeth komanso Kamuzu Central asanapume ntchito mu 2007 kamba ka matenda a shuga omwe anapangitsa kuti miyendo yawo iwiri idulidwe.
Chaka chatha nyumba ya mayi Tembo kwa Manase mumzinda wa Blantyre inagwa kamba ka namondwe wa Freddy ndipo katundu wawo wina anawonongeka. Kamba kakuchepekedwa banja lawo limakhalabe nyumba yomweyo.
Atamva za umoyo wa mayi Tembo kudzera kwa professor Address Malata, mayi Mpinganjira agulira mayiyu nyumba yamakono ya mtengo wa K30 miliyoni ku Chileka munzinda omwewu wa Blantyre kuphatikizapo katundu wina wa m’nyumbamo.
Poyankhula atapeleka nyumbayi Lachisanu, Mpinganjira wati “Mayiyu amafunika thandizo. Ndinakhudzidwa kwambiri nditava nkhani yawo kuti atatha kuthandiza anthu mzipatala, amavutika kwambiri.
Choncho ndinaona kuti nkwabwino ndithandize ndi nyumba yoti azikhala mosangalala ndipo ndikukhulupilira kuti moyo wake sukhala chimodzimodziso.”
Mpinganjira walimbikitsa anthu m’dziko muno kuti adzikhala ndi moyo ofuna kuthandiza ena ngakhaleso omwe siabale awo ponena kuti dziko lino litha kukhala labwino ngati aliyese atanyamula udindo othandiza anthu ovutika.
Mayi Tembo omwe amawoneka a chimwemwe chodzadza tsaya, ati kuyambira chaka cha 2007 pomwe anaima ntchito, moyo m’banja lawo wakhala ovutika kwambiri chifukwa iwowo ndi omwe amathandiza chili chose.
“Ndine wothokoza kwambiri chifukwa cha nyumba ya bwino yomwe ndapatsidwa. Pamoyo wanga sindinayembekezere kuti ndingadzakhale nyumba ya siling’i komanso matayilosi ngati ino. Mulungu awadalitse mayi Mpinganjira, a Malata komanso anthu onse omwe apangitsa kuti izi zitheke,” anatero mayi Tembo.
Nawo professor Malata ati ndiokondwa kwambiri kuti khumbo lawo lowona mayi Tembo akukhala moyo wabwino latheka ndipo ayamika a Mpinganjira komanso anthu onse omwe athandiza mayi Tembo.
Professor Malata apempha bungwe logulitsa magetsi la ESCOM kuti lichite machawi kupititsa magetsi ku nyumbayi kuti mayi Tembo azikwanitsa kusunga mankhwala a shuga omwe amamwa.