A Malawi ayembekezere nkhani zakathithi zakunyumba ya malamulo

Advertisement
Training- journalists

A Malawi ayembekezere nkhani zakathithi komanso zothyakuka bwino zokhudza zokambirana komanso zomwe zimachita m’nyumba ya malamulo pofuna kuonetsetsa kuti anthu m’dziko muno akutsatira bwino lomwe za momwe zinthu zimayendera m’nyumbayi.

Izi zikudza pomwe bungwe la Centre for Social Accountability and Transparency (CSAT) linachititsa maphunziro atolankhani pa 31 May ku Grand Palace Hotel mu mzinda wa Mzuzu.

Mwazina bungweli linaphunzitsa atolankhani za lamulo lovomeleza anthu kupeza mauthenga kuchokera kunyumba ya malamulo lomwe pachingerezi likutchedwa kuti Access to Information on Parliamentary Support Programe, ndipo anakambanso za momwe lamuloli limagwilira ntchito.

M’modzi mwa akatswiri ochokera ku bungwe la CSAT a Moffat Phiri anati maphunzirowa ndiwofunika kwambiri kamba kakuti athandizira kuchepeza mavuto ena omwe atolankhani amakumana nawo mdziko muno pankhani yofalitsa mauthenga ochokera ku nyumba ya Malamulo.

Maphunzirowa athandiziranso atolankhani kudziwa momwe angathanirane ndi mavuto omwe amakumana nawo akafuna kulemba nkhani zokhudzana ndi kunyumba ya malamulo.

Naye msungi chuma wagulu la atolankhani okhala ku mpoto la Nyika Media Club, Sarah Saulos anayamikira bungweli kamba kamaphunzirowa ponena kuti zithandizira atolankhani kudziwa za maufulu awo  akafuna kupeza mauthenga aku nyumbayi.

Advertisement