Amalawi ambiri ndi mbuli – watero muwulutsi wa pa Mibawa Chawezi Banda

Advertisement
DPP- members Njamba Rally

Unyinji unakhamukira ku Njamba lamulungu lija ati si chifukwa chokonda a Mutharika, kapena DPP, kapena kukhumudwa ndi kayendetsedwe ka dziko kamba ka utsogoleri wa Tonse. Ati vuto la onse aja ndi umbuli basi, monga amakhalira a Malawi ochuluka.

A Chawezi Banda omwe ndi muwulutsi pa wailesi ya kanema ya Mibawa ndiwo anena izi. Iwo amayankhula mu pologalamu ya Kandimverere yomwe amakhala pansi ndi a Deus Sandram, kapena kuti o’Bwande, ndi kumasakatula za mavuto a dziko lino.

Malinga ndi a Banda amene anthu ambiri awatafulira kuti iwo akuonjeza mu kuteteza kwawo kwa boma la Chakwera, a Malawi ochuluka ndi opanda nzeru ndipo zimawapangitsa kuti aziputsitsidwa ndi andale monga a Mutharika.

a Malawi ambiri ndi opanda nzeru – Banda.

“Ndisanene mobisabisa apa kapena kuchita mozemba, a Malawi ambiri ndi opanda nzeru kapena tinene kuti umbuli ndi ochuluka mu dziko muno,” iwo anatero.

Anapitirizanso kunena kuti mavuto a zachuma ndi kukwera kwa zinthu mu dziko muno apangitsa si a Chakwera, ati izi ziri pa dziko ponse kungoti kamba ka umbuli wadzadza mu mitu ya a Malawi sangazimvetse.

A Banda ati iwo adapita ku dziko la Amereka kumene adapezanso kuti anthu akulira ndi mitengo ya zinthu. Ndipo adaonjezera kuti ku misonkhano ya mabungwe oona za chuma cha pa dziko kumene iwo adapita, onse ananena kuti chuma chavuta pa dziko lonse.

Koma anthu ena oonela pologalamu imeneyi adadzudzula a Banda kuti akuyankhula mwa mtudzu ati kamba iwo ndi okonda Kongeresi chabe. Ena adaululanso kuti a Banda akupanga izi kamba koti akufuna kuyima ngati phungu wa chipani cha Kongeresi ku Ndirande. Izi, a Malawi24 sitinatsimikize.

Advertisement