“Ndiyimanso, ndipo ndiwinanso,” watero Chakwera

Advertisement
Chakwera

Inu nonse munadzadzana pa Njamba lamulungu, yang’anani kumbali. Ndipo inu mumayesa kuti 2025 ndi ya a Chilima, talikilani. Uthenga uli pano ndi wa onse okondwa ndi a Chakwera. Iwo ati 2025 ino akupitiriza, zotuluka m’boma muiwale.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera lero auza mtundu wa a Malawi kuti iwo ayimanso chaka chamawa ndipo apambananso. Iwo anena izi pa mwambo okumbukila a Kamuzu Banda mu mzinda wa Blantyre.

Malinga ndi a Chakwera, iwo ati anthu ayiwale zoti chaka chamawa achoka pa udindo chifukwa iwo akhala akupitiriza pomwe anasiyira. Iwo ati a Malawi asanyengeke ndi a ndale ofuna kugawa mitundu koma alunjike maso pa iwo basi.

Zolankhula za a Chakwera zikudza pomwe lamulungu lomweli a Peter Mutharika adali pa Njamba pomwe anauza a Chakwera kuti ayambe kupakira chifukwa iwo a Mutharika akubwelelanso m’boma.

Anthu ena akuyesa kuti alowanso m’boma, izi sizitheka, a Chakwera ayankha a Mutharika.

Zokamba za a Chakwera zitha kudabwitsa anthu ena otsatira a Chilima a UTM kamba koti akamuna awiriwa adamvana kuti mu chaka cha 2025 azachite cholandirana kuti a Chilima atsogole.

Advertisement