Malawi sakukwanitsa kusamalira atsogoleri ake akale – atero a Bakili Muluzi

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi ati chisamaliro cha atsogoleri opuma chomwe boma limapereka  chikufunika  kuunikidwanso, ponena kuti pali zigwelu zambiri zofunika kukonza .

Mtsogoleri wakaleyu wati, mwa chitsanzo, pakali pano amagwiritsa ntchito ndalama za mthumba mwake kugulira zakudya komanso mafuta a galimoto.

A Muluzi ati adalankhulapo ndi mlembi wamkulu wa boma, a Colleen Zamba za chisamaliro cha atsogoleri opuma ndipo ati a Zamba adavomeleza kuti malamulo a dziko lino pa chisamaliro cha atsogoleri opuma akufunika kuunikiridwanso.

Mtsogoleri opumayu anatinso mzokhudza kuti katundu akukwera mtengo kwambiri mdziko muno ndipo ati anthu ambiri akudandaula ndipo anati boma likuyenera kuteteza chuma cha dziko lino kuti anthu asapitilire kuvutika.

Polankhula mu pologalamu ya  Exclusive  Interview pa kanema ya Times, a Muluzi anawonjezera kuti atsogoleri opuma sakuyenela kudana kufika pokanika kulankhulana ponena kuti zimenezo mzopasula dziko.

“Anthu ena amakhala ndi chidani, amakhala ndi mkwiyo kwambiri timayenera tidziyankhulana tikatero tibweletsa umodzi. Atsogoleri amafunika azilankhulana, kusunga mangawa mzosapindula” anatelo a Muluzi.

Iwo anamaliza kunena kuti a Malawi apitilize kukondana ndipo demokalase isabweletse udani pakati pa a Malawi komanso kulekana  kwa makaka a zipani kusabweletse chisokonezo m’dziko muno.

A Muluzi adakhala mtsogoleri oyamba mu ulamuliro wa zipani zambiri kuchoka m’manja mwa a Hastings Kamuzu Banda, ndipo adatsogolera dziko lino pansi pa chipani cha United Democratic Front (UDF) kuyambira 1994 mpaka 2004.

Advertisement