Mlingo wa madzi mnyanja ya Malawi ukutsika

Advertisement

Patapita nthawi ma bizinezi ambiri atasokonekera mmbali mwa Nyanja ya Malawi kamba kakusefukila kwa madzi, a National Water Resources Authority (NWRA) ati tsopano mlingo wa madzi mu mnyanjayi ukuphwera.

Malingana ndi mneneri wa bungweli, a Masozi Kasambala izi zikudza kamba koti mvula yomwe imagwa ku Tanzania komanso mchigawo cha ku mpoto kwa dziko lino ikutsika.

“Ngati izi zingapitilire mlingowu upitilira kutsika kufikila mwezi wa Novermber pomwe timayamba chaka chatsopano pa nkhani ya kayendetsedwe ka madzi,” atero a Kasambala.

Masozi Kasambala, is spokesperson of National Water Resource Authority (NWRA),
Anthu akuyenera azitenga chilolezo asanayambe kumanga mmbali mwa nyanja – Kasambala.

Iwo anapitiriza kunena kuti sikoyamba kusefukila kwa madzi mmbali mwa nyanja ya Malawi kamba koti mchaka cha 1980 izi zidachitikanso.

“Titsimikize kuti mmene madzi anakwerera chaka chino ndichimodzimodzi mmene zinachitikila mchaka cha 1980,” anatsindika motero a Kasambala.

Mneneriyu watinso zomwe zachitika chaka chino zikuonetsa kuti madzi saiwala khwawa ndipo anthu akuyenera kukhala osamala akamagwira ntchito zawo mmbali mwa nyanja kapena mitsinje.

“Anthu asanayambe kumanga kapena kulima mbali mwa nyanja akuyenera kupempha chilorezo kwa bungwe la National Water Resources Authority malingana nkuti madzi akhonza kukwera kamba ka zifukwa zosiyanasiya,” anachenjeza motero a Kasambala.

Posachedwapa ma bizinesi ambiri omwe ali mmbali mwa Nyanja ya Malawi adatsekedwa kamba ka kusefukira kwa madzi mmaboma monga Mangochi, Salima, Nkhata-Bay ndi ena.

Advertisement