Sukulu ya Msiki iwomboledwa ndi ophunzira akale apa Mzuzu University

Advertisement

Sukula ya sekondale ya Msiki m’boma la Mzimba ikusimba lokoma potsatira thandizo lokwanira 4.3 miliyoni  lomwe lalandira kuchokera kwa ophunzira akale pa sukulu yaukachenjede ya Mzuzu. 

Masiku anayi apitawo,  ophunzira akale pa Mzuzu University anadzidzimutsa sukulu ya Msika ndi thandizo la mabuku olemberamo komanso  ndalama zimene zigwire ntchito ngati sukulu fizi kwa ana khumi ndi asanu. 

Gululi lomwe m’chingerezi limatchedwa Mzuzu University (MZUNI) Alumni Association, linasonkhetsa ndalama zokwana 4.3 miliyoni kuti lipereke thandizoli. 

Pa ndalamayi, 2.9 miliyoni inagwiritsidwa ntchito  pogulira ophunzira pa sukulu ya Msika mabuku. Ndalama yotsalayo inagwiritsidwa ntchito kulipilira  ophunzira khumi ndi asanu sukulu fizi. 

Pa mwamba pa izi, ophunzira a kale pa Mzuni analonjeza kudzalipilira sukulu fizi kwa  ophunzira yemwe adzachite bwino kwambiri pa mayeso a JCE a 2024 ,kwa zaka ziwiri. 

A Kenneth Nyirenda yemwe ndi mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya Msika wauza Malawi24 kuti thandizo lomwe laperekedwali libweretsa kusintha kwambiri pasukuluyi. 

A Nyirenda anatinso thandizo la sukulu fizi lithandiza kuchepetsa vuto la kujomba kwa ana kusukulu. 

A Nyirenda apemphanso boma komanso anthu akufuna kwabwino kuti atengepo gawo lothandiza sukuluyi imene ilibe labolotale  komanso ili kalikiliki kofuna kumalizitsa  zipinda zina zophunziliramo zomwe zidangoyambidwa. 

Sukulu yoyendera ya Msiki idayamba mchaka cha 2022. 

Advertisement