Ayi chonde pitani khomo la mtima wanga ndatseka- Watero Jetu

Advertisement
Jetu

Iyi ndi chorus ya nyimbo ya  oyimba otchuka otchedwa Jetu yomwe wangotulutsa kumene  maola ochepa apitawa.

Nyimboyi yomwe dzina lake ndi chakwaza, ikuonetsa kuti mzimayiyu anali ndi chibwenzi dzina lake John ndipo chinatha mosakhala bwino zomwe zinapangitsa kuti asweke mtima.

” Kale unandiuza suli ready za chikondi sizingatheke m’malo mwake mzanga  analowa fisi,” ikutero mbali ina ya nyimboyi.

Nyimboyi yapangitsa anthu kuti ayikonde potengera m’mene akuiyichemerera pa masamba a m’chezo monga Facebook.

Kupatura Facebook nyimboyinso ili pa YouTube  ndi ma likes okwana 11,000 komanso ndemanga zosachepera 3,000.

Jetu ndi oyimba wachizimayi yemwe wayamba kuyimba nyimbo posachedwapa ndipo anthu akumakonda nyimbo zake posatengera kuti ndi wachizimayi. 

Wakalamba wafuna ndi nyimbo ina yomwe oyimbayu anaimba ndipo inapangitsa kuti dzina lake lipite patali.

Oyimbayu amatsogoleredwa ndi m’dzukulu wake yemwe ataona luso lake, anatengapo gawo lomulimbikitsa kuti lusoli lipite patsogolo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.