Apolisi ayamba kunjata anthu ogulitsa mowa wa “Ambuye Tengeni”

Advertisement
Malawi 24 news logo

Kwachema kwa Manase ku Blantyre pamene apolisi ayamba kunjata anthu onse omwe akugulitsa mowa omwe ndi owopsa ndipo ukutchulidwa ndi mayina monga: Ambuye tengeni, magaga, komanso taya njinga omwe pakadali pano waphapo anthu asanu (5).

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’chigawo chakummwera, a Joseph Sauka, ati ntchitoyi ili mkati pamene apolisi afikakale kuderali komwe akulanda mowawu komanso kunjata ogulitsa chakumwachi.

A Sauka ati iwo monga apolisi ntchito yawo ndikuteteza anthu pa imfa zodza kaamba kakumwa chakumwa chomwe ndichosavomerezeka komanso chopereka chiwopsezo.

Pakadali pano anthu ena atatu ali m’chipatala kulandira thandizo atamwa mowawu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.