Nkhondo ya pa chiweniweni ya ku chipani chotsutsa cha DPP ikupitilira, tsopano akufuna kulikhirana ku malamulo a dziko. A Welani Chilenga amene anathotholedwa mu chipani limodzi ndi a Nankhumwa ati nkhalamba zisamayimire nawo pa zisankho.
Malinga ndi chikalata chimene Malawi24 yaona, a Chilenga ati iwo akufuna kusintha malamulo a dziko lino. Mu chikalatachi chimene chikupita kwa sipikala wa nyumba ya malamulo, a Chilenga ati pakufunika malamulo okhwima oletsa achikulire kuyimira pa maudindo.
“Polingalira kuti ma udindo oyendetsa dziko lino amafuna luntha komanso ndi olemetsa kwambiri, ndikuona kuti ndi bwino kuti anthu oyimira Mpando wa mtsogoleri wa dziko, wachiwiri wake komanso ngakhale a phungu azikhala ndi malire pa zaka,” atero a Chilenga.
A Chilenga afotokozanso mu chikalata chawo kuti pa ma udindo awa pamafunika anthu a nyonga zawo ndipo ndi chifukwa pakuyenera kukhala malire.
Koma akatswiri ena adabwa ndi malingaliro a bambo Chilenga amene akuona kuti angofuna kuthana ndi a Mutharika.
“Si za malamulo a dziko koma ndi ndewu basi, kufuna kuthana ndi a Mutharika,” watero Katswiri wina.
Asanachotsedwe ku chipani cha DPP, a Chilenga anali mbali ya a Kondwani Nankhumwa.