Flames ithambitsana ndi Chipolopolo lero pa Bingu Stadium

Advertisement

Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino Flames lero pa 26 March ikuyembekezereka kuthambitsana ndi Chipolopolo ya m’dziko la Zambia kulimbirana malo achitatu mu 4 Nations Tournament ndipo masewero ake ayamba 2 koloko masana.

Lero lomwe lino, Zimbabwe ikomana ndi Kenya kulimbirana malo woyamba ndipo masewero ake ayamba 5 koloko madzulo.

Zimbabwe inafika mu ndime yomaliza ya mpikisanowu itangonjetsa Zambia 6 – 5 kudzera m’mapenate ndipo Kenya inangonjetsa Malawi yomwe ndi mwini khomo 4 – 0 lasabata lapitali pa 24 March 2024.

Timu ya dziko lino yomwe ndi ya anyamata osapitilira zaka 20 (Under 20) inakhala akatswiri ampikisano omwewu koma osewera ake ali osapitirira zaka 20 itagonjetsa Zimbabwe 3-2 komanso Kenya 3-1 ndipo Kenya U20 inakhala nambala yachiwiri pamene Zimbabwe yachitatu koma sinapambane masewero aliwonse.

Matimu onse anayi akugwiritsa ntchito mpikisanowu pokonzekera mpikisano olimbirana malo mu mpikisano wa dziko lonse (FIFA World Cup Qualifiers) omwe ulipo mwezi wa June chaka chino.

Dzulo pa 25 March 2024, ma timu onse ochoka maiko anayiwa anabwera pamodzi pomwe anali ndi ntchito yobzala mitengo ku By-Pass mu mzinda wa Lilongwe motsogonzedwa ndi aphunzitsi awo, mtsogoleri wa FAM, Fleetwood Haiya komanso akuluakulu ena ochokera ku khonsolo ya Lilongwe.

Advertisement