Ku Neno kwabuka nthenda ya Rubella

Advertisement
Rubella Measles outbreak hits Neno District

Unduna wa Zaumoyo wati m’boma la Neno kwabuka nthenda yotchedwa Rubella yomwe yagwira anthu khumi ndi m’modzi.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe undunawu watulutsa lachisanu pa 23 March, 2024 yomwe asayinira ndi Dr Samson Mndolo omwe ndi mlembi wamkulu mu unduna wa zaumoyo

Undunawu wati pa 15 March chaka chino unalandira malipoti kuchokera ku Neno m’dera la Matope, mmudzi wa Manyenje kuti kumeneko akuganizira kuti kwabuka matenda a Chikuku ndipo 12 March 2024, adokotala a pachipatala cha Matope adapeza mwana wa miyezi 6 yemwe adali atatentha thupi, amatsokomola, anali atatuluka nsungu thupi Ionse, anali ofiira maso komanso anali ndi chimfine.

A chipatala atatenga zoyesa kwa mwanayu komanso anthu ena 15 omwe amakhala naye kuti zikapimidwe ku Chipatala chachikulu cha Kamuzu Central ku Lilongwe, zotsatila za zoyesazi zinatuluka pa 20h March, 2024.


Zotsatirazi zasonyeza kuti mwanayu komaso anthu onse omwe anayezedwawa, palibe yemwe amadwala nthenda ya Chikuku monga momwe amaganizira ndipo poti mwanayo sanali odwalika kwambiri, adamupatsa thandizo ndikulangiza makolo momwe angakakhalire naye mosamala kuti asapatsire matendawa kwa ena pamene anali kunyumba.

M’malo mwake, zotsatira za kufufuza mozama za matendawa, zasonyeza kuti mwa anthu 15 omwe anayezedwa, 11 apezeka ndi matenda a Rubella.

Undunawu wati wodwata matenda a Rubella amaonetsa zizindikiro zofanana ndi yemwe akudwala Chikuku ndipo wati chizindikiro chenicheni cha matenda a Rubella ndi tinsungu tomwe timayambira kunkhope makamaka kuseri kwa makutu kenako nkumafalikira mkhosi ndi thupi Ionse.

Pakadali pano undunawu wati palibe mankhwala enieni ochiza Rubella.

Rubella ndi matenda omwe amafala msangamsanga koma amatha okha pakamatha sabata koma wati ukuchita chothekera kuti matendawa asafale kwambiri.

“Pofuna kuonetsetsa kuti matendawa asapitilire kufala, unduna wa Zaumoyo mogwirizana ndi mabungwe wakhazikitsa ndondomeko zingapo. Mwa zina, boma la Neno lakonza kampeni yoti tipereke katemera wa Chikuku ndi Rubella mdera lomwe lakhudzidwa ndi matendawa.

“Pakadali pano tikuphunzitsa anthu kuti adziwe zambiri za matenda a Chikuku ndi Rubella. zizindikiro zake komanso kufunika kwa katemera wa Chikuku ndi Rubella. Tili pa kauniuni wofufuza enanso omwe angapezeke ndi matendawa, komanso kuti tidziwe madera omwe akhudzidwa kwambiri,” yatelo kalata ya undunawu.

Kupatula apo, undunawu wati ukupereka thandizo loyenera kwa onse amene apezeka ndi matendawa komanso wati ukulumikazananso ndi sukulu zonse m’derali ndi atsogoleri osiyanasiyana kuti agwirane manja pothetsa matendawa.

Njira zina zopewera matendawa ndi kukhara mwaukhondo monga kusamba m’manja ndi sopo, kutseka pakamwa potsokomola kapena kuyetsemula ndi polandira katemera.

Advertisement