Boma la Malawi kudzera ku nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno ya DICS, tsopano yakhazikitsa mtengo wa K50,000 ngati mtengo wa tsopano wa chiphaso choyendera cha anthu wamba.
Nkhaniyi ikudza pomwe nthambi ya DICS Lachitatu sabata yatha inalengeza kudzera mu kalata yomwe inatulutsa yosainidwa ndi mkulu wa nthambiyi a Brigadier Charles Kalumo, kuti boma latsitsa mtengo wa chiphaso choyendera cha anthu wamba ndi 55 kwacha pa 100 kwacha iliyonse.
Chikalatachi chinafotokoza kuti tsopano a Malawi omwe azipangitsa chiphaso choyendera kuyambira pano, akuyenera kumalipira K50,000 osatiso K90,000 yomwe nzika za dziko lino zakhala zikulipira mbuyo monsemu.
Lero Lolemba pa 18 March, 2024, boma kudzera ku nthambi ya DICS latulutsa chikalata chokhazikitsa mtengo watsopanowu zomwe zikutanthauza kuti anthu onse omwe angapangitse chiphaso kuyambira pano, adzilipira mtengo wa tsopanowu omwe ndi K50,000.
Chikalatachi chikusonyeza kuti chiphaso cha munthu wamba chokhala ndi masamba 36 chidzilipilidwa pa mtengo wa K50,000 kuchoka pa K90,000 ndipo anthu wamba omwe angafune chiphaso cha pompopompo, akuyenera kumalipira K120,000 osatiso K160,000 yomwe nzika zimalipira poyamba.
Kuwonjezera apo, nzika wamba zofuna kubwezeretsa chiphaso chotayika kapena choonongeka, zidzilipira K70,000 osatiso K150,000 pomwe ma dalaiva a ma thilaki omwe amapita kunja pafupi pafupi, adzilipira K50,000 akafuna kupangitsa chiphaso chawo.
Chiphaso cha anthu wamba koma chokhala ndi masamba 48, chili pa mtengo wa kale wa K130,000, koma chasintha ndi chiphaso cha ana chomwe ndi cha masamba 36 ndipo tsopano chidzilipilidwa pa mtengo wa K40,000 kuchoka pa K80,000 ndipo chiphaso cha pompo pompo cha ana chafika pa K80,000 kuchoka pa K120,000.
Kuwonjezera apo, chiphaso chongoyembekezera chomwe ndi cha masamba khumi ndi awiri (12), chidzilipilidwa pa mtengo wa K70,000 ndipo chiphaso cha akuluakulu a boma ndi ena chili pa mtengo wa kale omwe uja omwe ndi K200,000.