Achikulire ku Balaka ati tsopano akumalandira thandizo msanga ku chipatala

Advertisement
A Manesi Justin, omwe ali ndi zaka 83 zakubadwa ndipo amachokera m’mudzi mwa Kwitanda, mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka

A Manesi Justin, omwe ali ndi zaka 83 zakubadwa ndipo  amachokera m’mudzi mwa Kwitanda, mfumu yaikulu Nsamala m’bomali m’mbuyomu, achikulire amakumana ndi zipsinjo zadzaoneni akapita kukalandira chithandizo cha mankhwala kuchipatala. Gogoyu adawonjezera kuti izi zidali chonchi kaamba kakuti ogwira ntchito za umoyo ena samawalabadira achikulirewa.

Iwo ati tsopano achikulire okhala mozungulira zipatala za Kwitanda komanso Dziwe m’boma la Balaka akumalandira chithandizo cha chipatala msanga.

Izi zachitika kudzera mu polojekiti ya “Accountability on fulfillment for Older People to Raise their Dignity’’-AFFORD yomwe mgwilizano wa mabungwe a Malawi Network of Older Persons’ Organisation-MANEPO komanso Foundation for Civic Education and Social Empowerment-FOSECE limagwira m’dera la GVH Kwitanda komanso Mpilisi.

“Mu zaka zam’mbuyomu,  ife achikulire timakhala pa mzere mkumadikilira chithandizo cha mankhwala monga odwala wina aliyense. Koma masiku ano, ogwira ntchito za umoyo amatilemekeza potipatsa mwayi  oyambilira okumana ndi adotolo komanso kulandira chithandizo cha mankhwala mwachangu. Masiku ano, sitikhalanso pamzele monga kale,” adafotokoza gogo Justin.

Malingana ndi gogo Fanny Rajab a m’dera lomweli, nkhanza pakati pa achikulire zachepa chifukwa bungwe la MANEPO lakhala kalikiliki kugwira ntchito ndi , ma komiti owona za anthu achikulire m’midzi ndipo anthu awunikilidwa mokwanira za kuipa kochitira achikulire nkhanza.

Ndipo m’mawu ake, dotolo wamkulu pa chipatala cha Kwitanda a Chikumbutso malinga adati polojekiti ya AFFORD kudzera mu ma komiti oyang’anira anthu achikulire m’midzi,  yathandizira kuti ogwira ntchito za umoyo awunikilidwe komanso kuzindikilitsidwa za kufunika kolemekeza anthuwa powapatsa chithandizo cha mankhwala moyenelera komanso mwachangu.

“Tisanayambe ntchito m’mawa wina ulionse, timafotokozera odwala amene abwera kudzalandira chithandizo cha mankhwala pa chipatala chino kufunika kothandiza anthu achikulire moyambilira. Ndi zosangalatsa kuti anthuwa amachimvetsetsa chilinganizochi ndipo pano zangosanduka ngati chikhalidwe chathu,” adatero Malinga.

Mkulu oyang’anira ntchito zosiyanasiyana ku bungwe la MANEPO a Goodwell Thunga adatsindika kuti ndi kofunikira kwambiri kuti anthu m’dziko muno azizindikira kuti achikulire nawonso ali ndi ufulu ndipo akuyenera kuwalemekeza m’magawo osiyanasiyana.

A Thunga adafotokoza kuti  nthawi zina, ogwira ntchito zaumoyo m’dziko muno samadzipereka pakagwilidwe kawo ka ntchito zomwe zimapangitsa kuti achikulire asamalandile thandizo la makhwala moyenelera.

Iwo adamema atsogoleri a m’madera kuti azikhala patsogolo kumenyera ufulu wa anthu achikulire m’madera mwawo.

Mabungwe a MANEPO komanso FOCESE amagwira ntchitoyi m’madera a mfumu Kwitanda, Mpilisi komanso Nailuwa kuphatikizanso m’madera ena a boma la Blantyre.

Ntchitoyi imagwilidwa ndi thandizo la ndalama lochokera ku Irish Aid kudzera ku bungwe la HelpAge International.

MANEPO ndi mgwilizano wa mabungwe omwe si aboma oposa makumi asanu ndipo cholinga chake ndi kumenyera ufulu a anthu achikulire poonetsetsa kuti akukhala moyo olemekezeka komanso kulimbanandi nkhanza zomwe amakumana nazo.

Advertisement