Anjatidwa kamba kogwililira mtsikana  wa zaka 14

Advertisement

Apolisi ku Chileka mu mzinda wa Blantyre amanga bambo Paul Mugawa a zaka 50 zakubadwa powaganizira kuti amagonana ndi mtsikana wa za 14.

Mneneri wa apolisi ya Chileka, Jonathan Phillipo, wati a Mugawa anali pa ubwenzi ndi mtsinakayu kuyambila mwezi wa October chaka chatha.

A Phillipo anati :”Mai a mwanayu ndiye anadzapereka lipoti ku polisi atazindikira kuti mwana wawo ali pa ubwenzi ogonana ndi bamboyu.

“Ubwenzi wa awiriwa unayamba pamene mtsikanayu anapita kunyumba kwa a Mugawa kukasewera ndi mwana wawo wa mkazi”.

Apolisi atalandira dandaulori komaso umboni anatengera mwanayu ku chipatala cha QECH ndipo zotsatira za chipatala zaonetsa kuti mwanayu amagonana ndi munthu.

Pakanali pano Mugawa ali mchitokosi cha apolisi ndipo akuyembekezera kuyankha mulandu wogonana ndi mwana wa mkazi osakwana zaka 18 zakubadwa zomwe  zikutsutsana ndi gawo 138 la malamulo a dziko lino.

Wolemba: Peter Mavuto

Advertisement