Shammah Vocals wati mipingo ikhale patsogolo yolimbikitsa achinyamata zatsogolo labwino

Advertisement
Shammah Vocals Malawi

M’modzi mwa anthu oyimba mdziko muno Shammah Vocals wapempha mipingo kuti ikhale patsogolo yochititsa misonkhano ya achinyamata kuti idziwalimbikitsa zatsogolo labwino la moyo wao.

Shammah Vocals yemwe dzina lake leni leni ndi Shammah Sitola wayankhula izi ndi Malawi24 ku Malindi Secondary School ku Zomba pomwe adakayimba ndikusangalatsa achinyamata pa nsonkhano wamapemphero omwe udachititsa ndi mpingo wa Everlasting Life Missionary Church.

Shammah Vocals adati iye ngati wa achinyamata adakayimba kunsonkhanowo ndikusangalatsa achinyamata anzake komanso kuwalimbikitsa kuti aziyenda njira yolondola kuti akafikire zinthu zomwe umakhumbira mtima mwao.

Pamenepa, iye adapempha achinyamatawo kuti atsatire zomwe zakambidwa kunsonkhanowo popeza zonse zomwe zakambidwa ndizokhudza maphunziro awo komanso mtsogolo lawo.

“Ndidzofunika kwambiri kuti ife oyimba tidzibwera m’misonkhano ngati imeneyi pofuna kulimbikitsa achichepere omwe akubwera pambuyo pathu kuti nawonso adzitha kudzikhulupilira okha pazochita zawo,” anatero Shammah Vocals.

Iye adalonjedzanso kuti chaka chamawa adzaakhala nawonso pansonkhano wa achinyamatawa.

Advertisement