A Mike Mwawa alandila chilango mnyumba ya malamulo nthawi yothaitha

Advertisement

Phungu wa wa dela la ku mmwela cha kum’mawa m’boma la Salima a Mike Ng’ombe Mwawa awatulutsa m’nyumba ya malamulo ndipo ati adzabwere pa 13 malichi kamba ka kuyankhula zosayenera mnyumba ya malamulo mu zokambilana za dzulo.

Sipikala wa nyumbayi a Catherine Gotani Hara wati atakamvetsela zomwe a Mwawa anayankhula kudzela pa zotepedwa za m’nyumbayi zinaonetsadi kuti phunguyu adalankhuladi zosayenera.

A Gotani Hara ati khalidwe loyankhula mosakhala bwino komanso kugwiritsa ntchito mawu ena osaloredwa likuchulukira m’nyumba ya malamulo zomwe zikupeleka chithunzi choyipa kwa omvetsela zokambilanazi.

A Hara ati iwo sasekelera aliyense amene adzichita zosemphana ndipo adzitulutsidwa m’nyumbayI pogwiritsa ntchito ndondomeko yoyendetsela nyumbayi ya nambala 105.

A Mike Mwawa apatsidwa chilango chosabwera mnyumba ya malamulo kwa masiku awiri kuyambila pa 11 mpaka pa 13 March chaka chino.

Aphungu m’nyumbayi ayamba kuzukuta m’magulu (Clusters) kwa masabata awiri kuyambila lolemba mpaka pa 11 malichi ndipo a Mwawa awalola kuzukuta nawo ndondomeko ya zachuma mmasiku oyikikawa

Advertisement