GVH Makungula akuyimba lokoma chifukwa cha ng’ombe za mkaka komanso nkhuku za mazira

Advertisement
GVH Makungula akuyimba lokoma chifukwa cha ng'ombe za mkaka komanso nkhuku za madzira

Mfumu Makungula a mdera la T/A Nkagula Boma la Zomba akuyimba lokoma pakhomo pawo chifukwa akupha makwacha ndi ng’ombe za mkaka komanso nkhuku za mazira zomwe amaweta.

Poyankhula ndi Malawi24, GVH Makungula adati alindi ng’ombe zisanu ndi zitatu za mkaka ndiponso nkhuku ndipo mwezi uliwonse amatolera ndalama zotsachepera 2 million kwacha za mkaka komanso madzira.

Iwo adati ngati mfumu adayamba ulimi wang’ombe ndi nkhuku pofuna kuwonetsa chitsanzo chabwino kwa anthu awo kuti mfumu isamangokhala kudalira zolandira koma idzikhalanso yotakataka pakhomo pake kuti isamasowe chakudya komanso ndalama zolipilira ana sukulu.

GVH Makungula adati kudzera mu ulimi wang’ombe ndi nkhuku, iwo akukwanitsa kuwalipilira ana awo sukulu zogonera komweko za sekondale komanso adakwanitsa kugula filiji yayikulu yandalama zokwana 2.5 million kwacha momwe amasungira mkaka komanso zinthu zina zapakhomo.

“Kupatula kuweta ng’ombe za mkaka komanso nkhuku, ndimachekesanso madabwa omwe ndimagulitsa kwa omanga nyumba komanso kwa opala matabwa osiyana siyana ndipo ndithokoze mkazi wanga chifukwa ndiyemwe akumandithandidzira zinthu zambiri kuti ma buzinesi athu adzipita patsogolo.” adatero a GVH Makungula.

Ndipo poyankhulapo, mkazi wa GVH Makungula Mai Gloria Walawala adati pamene amayamba kuweta ng’ombe za mkaka zimawoneka ngati zachibwana popeza sankadziwa kuti muli phindu ndipo chifukwa chopeza ndalama zocholuka adaganizanso zoyamba kuweta nkhuku za madzira.

Mai Walala adati kudzera mu ulimi wa nkhuku, patsiku amatolera mazira ochuluka ndipo ali ndi maganizo owonjezera makola ankhuku pofuna kuti adziweta nkhuku zambiri.

Iwo adati mgwirizano omwe ulipo pakati pa iwo ndi amuna awo wothandizana ntchito zosamalira ng’ombe ndi nkhuku limodzi ndizomwe zikupangitsa kuti pakhomo pawo asamasowe ndalama komanso chokudya.

Advertisement